Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Zingatithandize Tikakhala ndi Nkhawa

Zimene Zingatithandize Tikakhala ndi Nkhawa

NKHAWA tingaziyerekezere ndi katundu wolemera ndipo zingachititse kuti tisakhale ndi mtendere wamumtima. (Miy. 12:25) Kodi munayamba mwavutikapo chifukwa chokhala ndi nkhawa pa moyo wanu? Kodi nthawi zina mumamva ngati simungathenso kupirira? Ngati ndi choncho dziwani kuti si inu nokha. Ambirife mwina tili ndi udindo wosamalira ena ake, anthu amene tinkawakonda anamwalira, tinakhudzidwa ndi ngozi zam’chilengedwe, kapenanso zinthu zina zomwe zachititsa kuti tisakhale ndi mphamvu komanso tizida nkhawa kwambiri. Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize kupirira tikakhala ndi nkhawa? *

Tingaphunzire zimene zingatithandize kupirira tikakhala ndi nkhawa, tikaganizira chitsanzo cha Mfumu Davide. Iye anakumana ndi mavuto ambiri pa moyo wake, nthawi zinanso kutsala pang’ono kufa. (1 Sam. 17:34, 35; 18:10, 11) Ndiye kodi n’chiyani chinkamuthandiza pamene ankada nkhawa? Nanga tingamutsanzire bwanji?

DAVIDE ANAKWANITSA KUPIRIRA PAMENE ANALI NDI NKHAWA

Davide anakumana ndi mayesero angapo pa nthawi imodzi. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitika pa nthawi ina pamene ankathawa Mfumu Sauli. Davide ndi amuna omwe anali nawo akuchokera kunkhondo anapeza kuti adani awo aba katundu wawo yense, awotcha nyumba zawo ndipo atenga akazi ndi ana awo ngati akapolo. Ndiye kodi Davide anatani? “[Iye] ndi anthu amene anali naye anayamba kulira mofuula mpaka kulefuka osathanso kulira.” Nkhawa yake inawonjezeka pomwe amunawa, omwe ankawadalira, anayamba “kukambirana zom’ponya miyala.” (1 Sam. 30:1-6) Pamenepatu Davide anakumana ndi mavuto akuluakulu atatu pa nthawi imodzi. Moyo wa anthu a m’banja lake unali pangozi, ankaopa kuti amuna omwe anali nawo amupha, komanso Mfumu Sauli inali ikupitirizabe kumufunafuna. Apatu Davide ayenera kuti anali ndi nkhawa kwambiri.

Kodi kenaka Davide anachita chiyani? Nthawi yomweyo “anadzilimbitsa mwa Yehova Mulungu wake.” Kodi anachita bwanji zimenezi? Nthawi zambiri iye ankakonda kupemphera kwa Yehova komanso kuganizira mmene Yehova anamuthandizirapo m’mbuyomo. (1 Sam. 17:37; Sal. 18:2, 6) Davide anaona kuti ayenera kupempha malangizo kwa Yehova choncho anafunsira kwa Yehova zimene ayenera kuchita. Yehova atamupatsa malangizo, iye anachitapo kanthu mwamsanga. Zotsatirapo zake n’zakuti iye ndi amuna omwe anali nawo, anadalitsidwa ndi Yehova ndipo analanditsa mabanja ndi katundu wawo. (1 Sam. 30:7-9, 18, 19) Kodi mwaona zinthu zitatu zimene Davide anachita? Anapemphera kwa Yehova, kuganizira mmene Yehova anamuthandizirapo m’mbuyomo komanso kutsatira malangizo amene anapatsidwa. Kodi tingamutsanzire bwanji? Taganizirani njira zitatu izi.

TIZITSANZIRA DAVIDE TIKAKHALA NDI NKHAWA

1. Muzipemphera. Nthawi iliyonse imene tili ndi nkhawa, tingapemphere kwa Yehova kuti atithandize komanso kutipatsa nzeru. Tikhoza kusiya kuda nkhawa popemphera kwa iye mochonderera ndi kumukhuthulira zonse za mumtima mwathu. Kapenanso tikhoza kupemphera mwachidule komanso mosatulutsa mawu potengera mmene zinthu zilili pa nthawiyo. Nthawi iliyonse pamene tapempha Yehova kuti atithandize, timasonyeza kuti timamudalira ngati mmene Davide ankachitira, yemwe anati: “Yehova ndiye thanthwe langa, malo anga achitetezo ndiponso Wopereka chipulumutso kwa ine. Mulungu wanga ndiye thanthwe langa. Ine ndidzathawira kwa iye.” (Sal. 18:2) Koma kodi pemphero limathandizadi? Mlongo wina dzina lake Kahlia, yemwe ndi mpainiya ananena kuti: “Ndikapemphera ndimapeza mtendere wamumtima. Pemphero limandithandiza kuti ndiziona zinthu mmene Yehova akuzionera ndipo ndimayamba kumudalira kwambiri.” Kunena zoona, pemphero ndi mphatso yayikulu yochokera kwa Yehova yomwe imatithandiza kulimbana ndi nkhawa.

2. Muziganizira mmene Yehova anakuthandizirani m’mbuyomo. Mukaganizira mmene zinthu zakhala zikuyendera pa moyo wanu, kodi pali mayesero amene munakwanitsa kuwapirira chifukwa chakuti Yehova anakuthandizani? Tikamaganizira mmene Yehova watithandizirapo komanso mmene anathandizira atumiki ake m’mbuyomo, timapeza mphamvu ndipo timayamba kumudalira kwambiri. (Sal. 18:17-19) Joshua yemwe ndi mkulu ananena kuti, “Sindimaiwala mapemphero anga amene anayankhidwa. Zimenezi zimandithandiza kukumbukira nthawi zimene ndakhala ndikupempha Yehova zinazake ndipo iye anandipatsa zimene ndinkafunikira.” Tikamaganizira mmene Yehova wakhala akutithandizira, timapeza mphamvu zotithandiza kulimbana ndi nkhawa.

3. Muzichitapo kathu. Tisanasankhe zochita pankhani inayake, tiyenera kufufuza malangizo odalirika m’Mawu a Mulungu. (Sal. 19:7, 11) Ambiri amaona kuti akafufuza mfundo za lemba lina lake, amayamba kumvetsa bwino mmene lembalo lingawathandizire pa moyo wawo. Jarrod yemwe ndi mkulu anafotokoza kuti: “Kufufuza kumandithandiza kuona mbali zosiyanasiyana za lemba lina lake komanso kumvetsa zimene Yehova akundiuza. Zimenezi zimandifika pamtima moti ndimatsatira malangizowo.” Tikamafufuza malangizo a Yehova m’Malemba komanso kuwatsatira, timakhala okonzeka kulimbana ndi nkhawa zimene tili nazo.

YEHOVA ADZAKUTHANDIZANI KUTI MUPIRIRE

Davide ankadziwa kuti ankafunika kuthandizidwa ndi Yehova kuti akwanitse kulimbana ndi nkhawa. Iye ankayamikira kwambiri mmene Yehova ankamuthandizira, mpaka anafika ponena kuti: “Ndi thandizo la Mulungu wanga ndingakwere khoma. Mulungu woona ndiye amandilimbitsa.” (Sal. 18:29, 32) Tikhoza kumaona mayesero amene tingakumane nawo ngati khoma limene sitingakwere. Koma ndi thandizo la Yehova, tingathe kulimbana ndi mayesero aliwonse okhala ngati makomawa. Choncho tikamapemphera kwa Yehova kuti atithandize, kuganizira zonse zimene watichitirapo m’mbuyomu komanso kutsatira malangizo ake, tingakhale otsimikiza kuti adzatipatsa mphamvu komanso nzeru zimene timafunikira kuti tilimbane ndi nkhawa.

^ Munthu amene akuda nkhawa kwambiri angafunike kuthandizidwa ndi achipatala.