Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chikondi chimatichititsa kuti tiziika zofuna za ena pamalo oyamba

Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Timakonda Anzathu?

Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Timakonda Anzathu?

Popeza kuti tinachokera kwa munthu mmodzi Adamu, tonse ndife banja limodzi. Ngakhale kuti anthu a m’banja limodzi amayenera kukondana komanso kulemekezana, masiku ano anthu sasonyezana chikondi choterechi. Mlengi wathu wachikondi safuna zimenezi.

ZIMENE MALEMBA OPATULIKA AMANENA PA NKHANI YA CHIKONDI

“Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”​—LEVITIKO 19:18.

“Pitirizani kukonda adani anu.”—MATEYU 5:44.

ZIMENE KUKONDA ANZATHU KUMATANTHAUZA

Onani mmene Mulungu anafotokozera chikondi m’Mawu ake opezeka pa 1 Akorinto 13:4-7:

“Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima.”

Taganizirani izi: Kodi mumamva bwanji anthu ena akamakuchitirani zinthu moleza mtima ndiponso mokoma mtima komanso ngati samakulusirani mukalakwitsa zinazake?

“Chikondi sichichita nsanje.”

Taganizirani izi: Kodi mumamva bwanji ngati anthu ena amangokukayikirani zilizonse kapena kukuchitirani nsanje?

Chikondi “sichisamala zofuna zake zokha.”

Taganizirani izi: Kodi mumamva bwanji ngati anthu ena amalemekeza maganizo anu ndipo samangokakamira maganizo awo okha?

Chikondi “sichisunga zifukwa.”

Taganizirani izi: Mulungu ndi wofunitsitsa kukhululukira anthu omwe achimwa n’kulapa. “Iye sadzakhalira kutiimba mlandu nthawi zonse chifukwa cha zolakwa zathu, kapena kutisungira mkwiyo mpaka kalekale.” (Salimo 103:9) Anthufe timasangala ngati munthu amene tamulakwira watikhululukira. Nafenso tizikhala okonzeka kukhululukira anthu amene atilakwira.​—Salimo 86:5.

Chikondi “sichikondwera ndi zosalungama.”

Taganizirani izi: Tikakumana ndi vuto linalake sitimafuna kuti anthu ena azisangalala. Choncho nafenso sitiyenera kusangalala anthu ena akakumana ndi mavuto, ngakhale kuti anthuwo sanatichitire zabwino.

Kuti Mulungu azitidalitsa, tiyenera kukonda ena posatengera msinkhu wawo, dziko limene akuchokera komanso chipembedzo chawo. Njira imodzi imene tingasonyezere chikondichi ndi kuthandiza ena.