Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tinalengedwa Kuti Tizikhala Kwamuyaya

Tinalengedwa Kuti Tizikhala Kwamuyaya

NDANI amene safuna kukhala ndi moyo wautali komanso wosangalala? Kodi mukuganiza kuti zikanakhala bwanji tikanakhala kuti timakhala ndi moyo wosangalala, wopanda matenda komanso wamuyaya? Bwenzi tikukhala nthawi yaitali ndi anthu amene timawakonda, tikanadziwa zambiri, kupita m’mayiko osiyanasiyana, kuphunzira kupanga zinthu komanso tikanakhala ndi nthawi yambiri yophunzira zinthu zimene zimatisangalatsa.

N’zosadabwitsa kuti anthufe timamafunitsitsa titakhala ndi moyo wamuyaya. Baibulo limati Mulungu anatipatsa mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale. (Mlaliki 3:11) Limanenanso kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Ndiye kodi zikanakhala zomveka kuti Mulungu atipatse mtima wofuna kukhala kwamuyaya, koma akudziwa kuti n’zosatheka kuti tikhale ndi moyo woterowo?

Kunena zoona, palibe amene amafuna kufa. Ndipotu Baibulo limati imfa ndi “mdani.” (1 Akorinto 15:26) Mdani ameneyu amatipeza ndithu anthufe. Ena amawapeza adakali ana pomwe ena amawapeza atakula. Ena akaganizira za imfa amachita mantha ndipo safuna n’komwe kuganizira za nkhaniyi. Ndiye kodi mdani ameneyu adzagonjetsedwa?

UMBONI WOTI MULUNGU SANKAFUNA KUTI TIZIFA

Kodi mukudziwa kuti sichinali cholinga cha Mulungu kuti anthu azifa? Buku la m’Baibulo la Genesis limasonyeza kuti cholinga cha Mulungu chinali choti anthu azikhala padzikoli kwamuyaya. Yehova Mulungu analenga dzikoli n’kuikapo chilichonse chofunika kuti anthu azikhalapo. Kenako analenga munthu woyamba, Adamu ndipo anamuika m’paradaiso, m’munda wa Edeni. Ndiyeno, “Mulungu anaona kuti zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambiri.”​—Genesis 1:26, 31.

Adamu analengedwa m’chifaniziro cha Mulungu ndipo anali wangwiro. (Deuteronomo 32:4) Nayenso Hava mkazi wake anali wangwiro. Yehova anawauza kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anire. Muyang’anirenso nsomba zam’nyanja ndi zolengedwa zouluka m’mlengalenga, komanso cholengedwa chilichonse chokwawa padziko lapansi.”​—Genesis 1:28.

Zikanatenga nthawi kuti Adamu ndi Hava limodzi ndi ana awo adzaze dziko lapansi. Pankafunika kuti Hava abereke ana, anawo n’kuberekanso ana, mpaka dziko lonse kudzaza ndi anthu ngati mmene Mulungu ankafunira. (Yesaya 45:18) Kunena zoona, Mulungu sakanauza Adamu ndi Hava kuti adzaze dziko lapansi akanakhala kuti anawalenga m’njira yoti adzamwalira akangokhala ndi ana komanso zidzukulu basi.

Komanso ganizirani za ntchito imene Mulungu anawapatsa yoti aziyang’anira zinyama. Mulungu anauza Adamu kuti apereke mayina kwa nyamazi ndipo zimenezi ziyenera kuti zinatenga nthawi. (Genesis 2:19) Koma kuti akwanitse kuziyang’anira bwino pankafunika kuti adziwe bwino nyama iliyonse komanso adziwe mmene angamaisamalire. Zimenezi zikanatenga nthawi yaitali kwambiri.

Choncho zimene Mulungu anauza Adamu ndi Hava zoti adzaze dziko lapansi komanso aziyang’anira zinyama, ndi umboni wakuti iye ankafuna kuti anthuwa akhale ndi moyo wamuyaya. Ndipotu tikayerekezera ndi moyo wa masiku ano, Adamu anakhala ndi moyo kwa nthawi yaitali.

CHOLINGA CHA MULUNGU NDI CHOTI ANTHU ADZAKHALE NDI MOYO KWAMUYAYA M’PARADAISO PADZIKO LAPANSI

ANAKHALA NDI MOYO KWA NTHAWI YAITALI

Adamu, zaka 930

Metusela, zaka 969

Nowa, zaka 950

Masiku ano, zaka 70-80

Baibulo limasonyeza kuti poyamba anthu ankakhala ndi moyo wautali kusiyana ndi masiku ano. Limati: “Masiku onse amene Adamu anakhala ndi moyo anakwana zaka 930, kenako anamwalira.” Kenako limatchula anthu enanso 6 amene anakhala ndi moyo zaka zoposa 900. Anthu ake ndi Seti, Enosi, Kenani, Yaredi, Metusela ndi Nowa. Anthu onsewa anakhalako Chigumula chisanachitike ndipo pamene Chigumula chinkachitika n’kuti Nowa ali ndi zaka 600. (Genesis 5:5-27; 7:6; 9:29) Kodi zinkatheka bwanji kuti anthu azikhala ndi moyo wautali chonchi?

Anthu onsewa anakhala ndi moyo pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Adamu ndi Hava anasiya kukhala angwiro. Chimenechi ndiye chifukwa chake anthuwa anakhala ndi moyo wautali. Koma kodi pali kugwirizana kotani pakati pa kukhala wangwiro ndi kukhala ndi moyo wautali? Nanga kodi imfa idzagonjetsedwa bwanji? Kuti tipeze mayankho a mafunso amenewa, tikufunika tidziwe kaye chifukwa chake anthufe timakalamba komanso kufa.