Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chiyani Chingakuthandizeni Kuti Musamakhale Mwamantha?

N’chiyani Chingakuthandizeni Kuti Musamakhale Mwamantha?

MWANA akangobadwa kumene amafunika kutetezedwa kwambiri ndi makolo ake. Ndipo akamayamba kukula amadziona ngati nyerere akadziyerekezera ndi akuluakulu. N’chifukwa chake amaopa kwambiri akaona anthu, koma akakhala ndi makolo ake, sachita mantha ndipo amaona kuti amuteteza.

Mwana amakula bwino makolo ake akamamukonda komanso kumulimbikitsa. Zimenezi zimathandiza kwambiri mwanayo kuti asamakhale mwamantha. Ndipo akachita zinazake zabwino makolo ake n’kumuyamikira, zimamuthandiza kuti apitirize kuchita zabwinozo.

Ndiyeno akayamba kusewera amapeza anzake amenenso amamuthandiza kuti asamachite mantha. Anzakewo amamuthandizanso kuti azolowere mwamsanga moya wa kusukulu.

Zimene tafotokozazi n’zimene zimachitikira ana ambiri. Koma ana ena sakhala ndi anzawo ambiri ndipo enanso sathandizidwa kwambiri ndi makolo awo. Mtsikana wina dzina lake Melissa * anati: “Ndikaona zithunzi za ana ena akusangalala ndi makolo awo, ndimalakalaka nanenso ndikanakhala ndi moyo umenewu pa nthawi yomwe ndinali mwana.” Kodi nanunso mumamva choncho?

MAVUTO OMWE AMAKHALAPO CHIFUKWA CHOKULA MWAMANTHA

N’kutheka kuti pamene munkakula munkadziderera chifukwa chakuti makolo anu sankakukondani kapenanso kukulimbikitsani. Mwinanso makolo anu ankangokhalira kumenyana mpaka banja lawo kutha ndipo munkadziimba mlandu kuti inuyo ndi amene munachititsa kuti banja lawo lithe. N’kuthekanso kuti vuto lalikulu kwambiri linali loti mayi kapena bambo anu ankakuchitirani nkhanza monga kusakuyankhulani bwino ngakhalenso kukumenyani kwambiri.

Kodi mavuto ngati amenewa amakhudza bwanji moyo wa mwana? Ana ena amayamba kumwa mowa mwauchidakwa komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Enanso amalowa m’magulu a zigawenga n’cholinga choti apeze anthu ocheza nawo. Ndipo ena amayamba zibwenzi kapena kulowa m’banja n’cholinga choti apeze anthu omwe angawamvetse ndi kuwakonda. Komabe zibwenzi ndi mabanja oterewa sizichedwa kutha ndipo zikatha mavutowo amangowonjezereka.

Ana ena sachita kufika polowerera chonchi, komabe nthawi zina amadziona ngati osafunika ngakhale kuti amayesetsa kupirira mavuto awo. Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Ana, ananena kuti: “Mayi anga ankakonda kundinena kuti ndine wachabechabe ndipo nanenso ndinayambadi kudziona choncho. Palibe tsiku limene anandiyamikirapo kapena kundichitira zinthu zosonyeza kuti amandikonda.”

Pali zinthu zinanso zimene zimapangitsa anthu ena kumadziona ngati osafunika. Zinthu zake ndi monga kutha kwa banja, ukalamba komanso kudziona ngati osaoneka bwino. Zinthu zimenezi zingapangitse kuti tisamasangalale komanso kuti tisamagwirizane ndi ena. Ndiye kodi tingatani kuti zinthu zimene tatchulazi zisatipangitse kudziona kuti ndife osafunika?

MULUNGU AMATIGANIZIRA KWAMBIRI

Baibulo limasonyeza kuti Mulungu angatithandize kuthana ndi maganizo amenewa.

Kudzera mwa mneneri Yesaya, Mulungu anati: “Usachite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.” (Yesaya 41:10, 13) Mavesiwa akusonyeza kuti sitiyenera kuda nkhawa kwambiri chifukwa Mulungu ndi wokonzeka kutigwira dzanja. M’mawu ena, tinganene kuti Mulungu ndi wokonzeka kutithandiza ngati timadziona kuti ndife osafunika.

M’Baibulo muli nkhani za anthu ena omwe ankada nkhawa kwambiri. Koma atapemphera, Mulungu anawathandiza. Mwachitsanzo, Hana yemwe anadzakhala mayi a Samueli, poyamba ankadziona ngati wosafunika chifukwa choti anali wosabereka. Mkazi mnzake ankakonda kumunyoza chifukwa cha vuto lakeli. Zimenezi zinkachititsa kuti Hana asamadye komanso azingolira. (1 Samueli 1:6, 8) Koma atapemphera kwa Mulungu, nthawi yomweyo anasiya kuda nkhawa.—1 Samueli 1:18.

Nayenso Davide ankakhala mwamantha nthawi zina. Kwa zaka zambiri, ankangokhalira kuthawathawa chifukwa Mfumu Sauli inkafuna kumupha. Maulendo angapo anatsala pang’ono kuphedwa ndipo anafika poona kuti mavutowo anali oposa msinkhu wake. (Salimo 55:3-5; 69:1) Komatu ngakhale anakumana ndi mavutowa, analemba kuti: “Ndidzagona pansi ndi kupeza tulo mu mtendere, Pakuti inu nokha Yehova mumandichititsa kukhala wotetezeka.”—Salimo 4:8.

Pa nthawi imene Davide ndi Hana anali ndi nkhawa, anapezanso mtendere atapemphera kwa Yehova kuti awathandize. (Salimo 55:22) Ndiye kodi tingawatsanzire bwanji?

MFUNDO ZITATU ZOTHANDIZA KUTI MUSAMADZIONE NGATI WOSAFUNIKA

1. Muzidalira kwambiri Yehova yemwe ndi atate wathu.

Yesu amafuna kuti tidziwe bwino Atate ake omwe ndi “Mulungu yekhayo amene ali woona.” (Yohane 17:3) N’zothekadi kumudziwa bwino chifukwa mtumwi Paulo analemba kuti Mulungu “sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Machitidwe 17:27) Nayenso Yakobo anati: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”—Yakobo 4:8.

Kudziwa kuti tili ndi Atate wathu wakumwamba amene amatikonda komanso kutiganizira kungatithandize kuti tisamakhale ndi nkhawa. N’zoona kuti kudalira Mulungu sikumangochitika lero ndi lero. Komabe anthu ambiri amaona kuti kudalira Mulungu n’kothandiza kwambiri. Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Caroline, anati: “Ndinayamba kuona Yehova ngati bambo anga moti ndinkamuuza chilichonse chomwe chinkandivutitsa maganizo. Ndikachita zimenezi, ndinkamvako kupepuka mumtimamu.”

Mtsikana winanso, dzina lake Rachel anati: “Pa nthawi imene makolo anga anamwalira, Yehova anandithandiza kwambiri kuti ndisamadzione ngati wosafunika. Ndinkamuuza zakukhosi kwanga komanso mavuto amene ndinkakumana nawo ndipo ankandithandiza.” *

2. Muzicheza ndi anthu amene amakonda Mulungu.

Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azionana ngati abale ndi alongo. Anawauza kuti: “Nonsenu ndinu abale.” (Mateyu 23:8) Yesu ankafuna kuti otsatira akewa azikondana n’kumagwirizana kwambiri ngati banja limodzi.—Mateyu 12:48-50; Yohane 13:35.

M’mipingo ya Mboni za Yehova anthu amayesetsa kukondana komanso kulimbikitsana ndipo amachita zinthu ngati banja limodzi. (Aheberi 10:24, 25) Anthu ambiri amaona kuti kupita kumisonkhano ya Mboni za Yehova kumawathandiza kuti asamakhale ndi nkhawa.

Mtsikana wina dzina lake Eva anati: “Ndinali ndi mnzanga winawake mumpingo wathu yemwe ankamvetsa bwino mavuto amene ndinkakumana nawo. Ndikamamufotokozera nkhawa zanga ankandimvetsera, kundiwerengera mavesi a m’Baibulo ndiponso kupemphera nane limodzi. Ankayesetsa kumandichezetsa kuti ndisamakhale ndi nkhawa. Ndimayamikira kwambiri zimene ankandichitirazi chifukwa zandithandiza kuti ndisamadzione ngati wosafunika.” Nayenso Rachel yemwe tamutchula kale uja, ananena kuti: “Ngakhale kuti makolo anga anamwalira, ndinapezanso amayi ndi abambo mumpingo wathu ndipo amandikonda komanso kundithandiza kwambiri.”

3. Muzikonda ena ndi kuwachitira zabwino.

Anthu akamakondana komanso kuchitirana zabwino, m’pamene amagwirizana kwambiri. Pa nkhani imeneyi, Yesu anati: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Zimenezi zikutanthauza kuti, tikamakonda kwambiri anthu, nawonso amayamba kutikonda kwambiri. Yesu anauzanso ophunzira ake kuti: “Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani.”—Luka 6:38.

Munthu akamakondana kwambiri ndi ena sakhala ndi nkhawa ndipo zinthu zimamuyendera bwino. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Chikondi sichitha” kapena kuti sichilephera. (1 Akorinto 13:8) Mayi wina, dzina lake María anati: “Panopa ndazindikira kuti si bwino kudziona kuti ndine wosafunika. Ndiye ndikangoyamba kudziona kuti ndine wosafunika, nthawi yomweyo ndimasiya n’kuyamba kuganizira mmene ndingathandizire ena. Ndikamathandiza ena, ndimamva bwino kwambiri mumtimamu.”

POSACHEDWAPA ANTHU ONSE SADZADANSO NKHAWA

Mfundo zimene takambiranazi sizingathetseretu vutoli koma n’zothandiza kwambiri. Caroline anati: “Ngakhale kuti nthawi zina ndimakhala ndi nkhawa, sindimadziona ngati wosafunika. Ndimadziwa kuti Mulungu amandikonda kwambiri. Ndilinso ndi anzanga omwe amandithandiza kuti ndisamade nkhawa.” Rachel nayenso ananena kuti: “Nthawi zina ndimakhumudwa ndi zinthu zina. Koma ndimasangalala kwambiri kuti abale ndi alongo anga amandilimbikitsa ndiponso kundithandiza kuti ndisamangoganizira za mavuto anga. Chosangalatsa kwambiri n’choti, tsiku lililonse, ndimapemphera kwa Yehova, yemwe ndi Atate wanga wakumwamba.”

Baibulo limasonyeza kuti m’dziko lapansi latsopano, mavuto onse adzatheratu. Pa nthawi imeneyo, anthu onse azidzakhala mwamtendere ndipo sipadzapezeka munthu woda nkhawa

Komanso, Baibulo limasonyeza kuti m’dziko lapansi latsopano, mavuto onse adzatheratu. Pa nthawi imeneyo, anthu onse sadzakhala mwamantha kapena kuda nkhawa. Baibulo limalonjeza kuti: “Aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu ndipo sipadzakhala wowaopsa.” (Mika 4:4) Palibe munthu amene azidzatiopseza kapena kutichitira zinthu zoipa. Ndipo zoipa zonse zimene zikutichitikira panopa “sizidzabweranso mumtima.” (Yesaya 65:17, 25) Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Khristu Yesu, adzachititsa kuti padzikoli pakhale “chilungamo chenicheni” ndipo kenako padzakhala “bata ndi mtendere mpaka kalekale.”—Yesaya 32:17.

^ ndime 5 Tasintha mayina onse m’nkhaniyi.

^ ndime 21 A Mboni za Yehova amaphunzira Baibulo ndi anthu kwaulere ndipo akhoza kukuthandizani kuti nanunso muzichita zimene Mulungu amasangalala nazo.