Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mayesero

Mayesero

Mayesero angachititse kuti mabanja athe, angasokoneze thanzi la munthu komanso angachititse munthu kuvutika ndi chikumbumtima. Ndiye kodi tingapewe bwanji mayesero?

Kodi kuyesedwa n’kutani?

Munthu amayesedwa akakopeka ndi zinazake makamaka zikakhala zolakwika. Mwachitsanzo, tiyerekezere kuti muli mu shopu ndiye mwaona chinthu chinachake ndipo mwakopeka nacho. Kenako mukuyamba kuganiza kuti mukhoza kuba chinthucho chifukwa palibe amene akukuonani. Koma mukuona kuti chikumbumtima chanu chikukuletsani. Ndiyeno mukuchotsa maganizo olakwikawo. Pamenepa tinganene kuti mwapambana mayesero.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

 

Munthu akakumana ndi mayesero sizitanthauza kuti ndi woipa. Baibulo limasonyeza kuti anthu onse amakumana ndi mayesero. (1 Akorinto 10:13) Koma chofunika kwambiri ndi zimene timachita tikakumana ndi mayeserowo. Anthu ena amaganizira kwambiri za zinthu zolakwika ndipo kenako amazichita. Pamene ena akayamba kuganiza zinthu zolakwika amazichotsa mwamsanga m’maganizo mwawo.

“Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako chake.”​—Yakobo 1:14.

N’chifukwa chiyani timafunika kuchitapo kanthu mwamsanga tikakumana ndi mayesero?

Baibulo limafotokoza zimene zimachitika kuti munthu afike pochita zoipa. Lemba la Yakobo 1:15 limati: “Chilakolako [cholakwika] chikatenga pakati, chimabala tchimo.” Mwachidule tingati munthu akamaganizira kwambiri zinthu zolakwika, amafika poti sangathe kudziletsa mpaka atachita zoipazo. Komabe ngakhale zili choncho, n’zotheka kupewa zilakolako zoipa.

MMENE BAIBULO LINGATITHANDIZIRE

 

Popeza munthu amachita kuika maganizo olakwika mumtima mwake, n’zothekanso kuwachotsa. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Maganizo olakwika akabwera tiziyamba kuganizira zinthu zina zabwino. Tikhoza kupeza ntchito imene tingagwire kapena kupita kukacheza ndi mnzathu. (Afilipi 4:8) Tingachite bwinonso kuganizira mavuto amene tingakumane nawo tikagonja pa mayeserowo. Mavutowa angakhudze thanzi lathu komanso ubwenzi wathu ndi Yehova. (Deuteronomo 32:29) Pemphero lingatithandizenso kwambiri. Paja Yesu Khristu anati: “Pempherani kosalekeza kuti musalowe m’mayesero.”​—Mateyu 26:41.

“Musanyengedwe, Mulungu sapusitsika. Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho”​—Agalatiya 6:7.

Kodi tingatani kuti tipambane polimbana ndi mayesero?

ZOONA ZAKE

 

Mayesero ali ngati msampha umene ungakole munthu wopusa komanso wosaganiza bwino. Nthawi zambiri mayeserowa amakhala okhudza chiwerewere ndipo angabweretse mavuto aakulu.​—Miyambo 7:22, 23.

MMENE BAIBULO LINGATITHANDIZIRE

 

Yesu Khristu anati: “Tsopano ngati diso lako lakumanja limakuchimwitsa, ulikolowole ndi kulitaya.” (Mateyu 5:29) Apa sikuti Yesu ankanena zochotsa diso lenileni. Koma ankatanthauza kuti ngati tikufuna kusangalatsa Mulungu komanso kudzapeza moyo wosatha, tiyenera kuchititsa ziwalo zathu kukhala zakufa pa nkhani yochita zinthu zoipa. (Akolose 3:5) Izi zikutanthauza kuti tiyenera kukana mwamsanga mayesero aliwonse. Popemphera kwa Mulungu, munthu wina wokhulupirika ananena kuti: “Chititsani maso anga kuti asaone zinthu zopanda pake.”​—Salimo 119:37.

N’zoona kuti nthawi zina kudziletsa kumakhala kovuta chifukwa choti “thupi ndi lofooka.” (Mateyu 26:41) N’chifukwa chake nthawi zina tingalakwitse zinthu. Komabe tikalapa n’kuyesetsa kuti tisabwerezenso zimene tinalakwitsazo, Yehova Mulungu adzatikhululukira chifukwa iye ndi “wachifundo ndi wachisomo.” (Salimo 103:8) Zimenezitu n’zolimbikitsa kwambiri.

“Inu Ya, mukanakhala kuti mumayang’anitsitsa zolakwa, ndani akanaima pamaso panu, inu Yehova?”​—Salimo 130:3.