Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 6

Muziwaphunzitsa Kufunika Kokhala ndi Makhalidwe Abwino

Muziwaphunzitsa Kufunika Kokhala ndi Makhalidwe Abwino

KODI MUNTHU WAMAKHALIDWE ABWINO AMATANI?

Anthu omwe ali ndi makhalidwe abwino amatha kusiyanitsa zabwino ndi zoipa. Mfundo zimene amatsatira sizimasinthasintha potengera mmene akumvera pa nthawiyo, koma ndi zimene amayendera nthawi zonse ngakhale pamene ali kwaokha.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUKHALA NDI MAKHALIDWE ABWINO N’KOFUNIKA?

Ana amaphunzira makhalidwe oipa kuchokera kwa anzawo akusukulu, nyimbo, mafilimu komanso mapulogalamu a pa TV omwe amaonera. Izi zimachititsa kuti azikayikira ngati kukhala ndi makhalidwe abwino n’kothandizadi.

Zimenezi zimachitika kwambiri pamene ana ali ndi zaka 13 mpaka 19. Buku lina linati: Pa nthawiyi, “ana amatengera zimene anzawo amachita komanso zimene amaonera kuti asaoneke otsalira. Choncho amafunika kuphunzira kusankha okha zochita pogwiritsa ntchito mfundo zimene amaphunzira, ngakhale zitakhala kuti anzawo onse sangasangalale nazo.” (Beyond the Big Talk) Apatu n’zoonekeratu kuti makolo ayenera kuyamba kuphunzitsa ana awo adakali aang’ono.

MUNGAPHUNZITSE BWANJI ANA ANU MAKHALIDWE ABWINO?

Muziwauza mfundo zoti aziyendera.

MFUNDO YA M’BAIBULO: ‘Anthu okhwima mwauzimu, amagwiritsa ntchito mphamvu zawo za kuzindikira, . . . kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.’​—Aheberi 5:14.

  • Muziwathandiza kudziwa zoyenera ndi zosayenera. Tsiku lililonse muzigwiritsa ntchito mawu owathandiza kudziwa zoyenera ndi zosayenera. Mwachitsanzo, mungawauze kuti: “Uku ndi kukhulupirika, uku ndi kusakhulupirika.” “Uku ndi kumvera, uku ndi kusamvera.” “Wachita zinthu mwachifundo, wachita zinthu mopanda chifundo.” M’kupita kwa nthawi, mwana wanu sangamavutike kudziwa zinthu zoyenera kuchita.

  • Muziwathandiza kudziwa mavuto amene angakumane nawo ngati atachita zoipa. Mwachitsanzo mungawafunse kuti: N’chifukwa chiyani kukhulupirika n’kofunika kwambiri? Kodi kunama n’koipa bwanji? N’chifukwa chiyani sitiyenera kuba? Mafunsowa angamuthandize mwana wanuyo kudziwa kuipa kochita zinthu ngati zimenezi.

  • Muziwauza kufunika kokhala ndi makhalidwe abwino. Mungauze mwana wanu kuti: “Ngati utamapewa kuchita zachinyengo anthu akhoza kumakukhulupirira,” kapena “Ngati utakhala wokoma mtima anthu angamakukonde.”

Anthu aziona kuti aliyense m’banja lanu ali ndi makhalidwe abwino.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Pitirizani kudziyesa kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani.”​—2 Akorinto 13:5.

  • Aliyense ayenera kukhala ndi makhalidwe abwino kuti muzinena ndi mtima wonse kuti m’banja mwathu:

    • “Sitinama.”

    • “Sitimenyana kapena kukalipirana.”

    • “Sitilankhula mawu achipongwe kapena kutukwana.”

Mukamachita zimenezi ana anu adzaona kuti sikuti iwowo ndi amene amangofunika kutsatira malamulo ena ake koma banja lanu lonse limatsatira mfundo zamakhalidwe abwino.

  • Muzikambirana ndi ana anu pafupipafupi mfundo zimene mukufuna kuti banja lanu lizitsatira. Muziwaphunzitsa pogwiritsa ntchito zochitika zatsiku ndi tsiku. Mwachitsanzo, mungayerekezere mfundo zamakhalidwe abwino zimene mumatsatira ndi zimene zimachitika kusukulu kapena zomwe zimaonetsedwa pa TV. Ndiye mungafunse mwana wanu kuti: “Kodi ukanakhala iweyo ukanatani?” kapena “Kodi banja lathu likanachita bwanji pamenepa?”

Muziwalimbikitsa kuchita zoyenera.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Khalani ndi chikumbumtima chabwino.”​—1 Petulo 3:16.

  • Muziwayamikira akasonyeza khalidwe labwino. Akasonyeza khalidwe labwino muzimuyamikira n’kumufotokozera chifukwa chake mukunena kuti wachita bwino. Mwachitsanzo mungamuuze kuti: “Unachita zinthu moona mtima. Ndiwe mwana wabwino.” Ngati mwana wanu wakuuzani kuti analakwitsa zinazake, muziyamba mwamuyamikira chifukwa chokuuzani zoona. Ndiyeno mungamuthandize kuti asadzachitenso zimene analakwitsazo.

  • Muziwadzudzula akamachita makhalidwe oipa. Muziwaphunzitsa kuvomereza zimene alakwitsa. Ana ayenera kudziwa zimene alakwitsa komanso kuti zochita zawozo zikusemphana ndi mfundo zimene banja lanu limatsatira. Makolo ena sauza ana awo kuti alakwitsa poopa kuwakhumudwitsa. Koma kukambirana ndi mwana wanu zokhudza khalidwe loipa limene wachita, kungamuthandize kudziwa chifukwa chake zomwe anachitazo zili zoipa komanso kuti asadzabwerezenso.