Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUNGATANI KUTI MUZIKHALA WOSANGALALA?

Kukhala Wokhutira Komanso Wopatsa

Kukhala Wokhutira Komanso Wopatsa

MWINA NTHAWI ZAMBIRI MUMAMVA ANTHU AKUNENA KUTI CHILICHONSE CHIMAKUYENDERA UKAKHALA NDI CHUMA. Maganizo amenewa amachititsa anthu ambiri kugwira ntchito maola ambiri kuti apeze chuma. Koma kodi ndi zoona kuti munthu amakhala wosangalala akakhala ndi ndalama komanso katundu? Tiyeni tione zimene ochita kafukufuku anapeza.

Magazini ina inanena kuti, ndalama si zimene zimachititsa munthu kukhala wosangalala. Koma ngati munthuyo ali ndi zinthu zofunika kwambiri pa moyo ndi pamene amakhala wosangalala komanso kukhala ndi mtendere wamumtima. (Journal of Happiness Studies) Magazini ina inanenanso kuti, “Ndalama pazokha zilibe vuto. Koma kufunafuna ndalama n’kumene kumachititsa munthu kukhala wosasangalala.” (Monitor on Psychology) Zomwe magaziniwa ananena zikugwirizana ndi zimene Baibulo linanena pafupifupi zaka 2,000 zapitazo. Linanena kuti: “Pakuti kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse, ndipo pokulitsa chikondi chimenechi, ena . . . adzibweretsera zopweteka zambiri pathupi lawo.” (1 Timoteyo 6:9, 10) Kodi ndi zopweteka ziti zomwe anthu ofunafuna chuma amakumana nazo?

NKHAWA KOMANSO KUSOWA TULO POFUNA KUTETEZA CHUMA Baibulo limati: “Wotumikira munthu wina amagona tulo tokoma ngakhale adye zochepa kapena zambiri. Koma zambiri zimene munthu wolemera amakhala nazo zimamulepheretsa kugona.”​—Mlaliki 5:12.

KUKHUMUDWA AKALEPHERA KUPEZA MTENDERE WOMWE AMAYEMBEKEZERA Chinthu china chomwe chimachititsa kuti anthu omwe amafunafuna ndalama azikhumudwa n’chakuti, ngakhale ndalamazo atazipeza sakhutira nazo. Ndipo Baibulo limati: “Munthu wokonda siliva sakhutira ndi siliva, ndipo wokonda chuma sakhutira ndi phindu limene amapeza.” (Mlaliki 5:10) Chinanso n’chakuti munthu akamafunafuna kwambiri chuma amanyalanyaza zinthu zofunika kwambiri zomwe zikanamuthandiza kukhala wosangalala. Mwachitsanzo, sapeza nthawi yocheza ndi banja lake, anzake komanso yotumikira Mulungu.

KUSOKONEZEKA MAGANIZO CHIFUKWA CHA KULOWA PANSI KWA BIZINEZI KAPENA CHUMA Baibulo limafotokoza kuti: “Usamadzitopetse ndi ntchito kuti upeze chuma. Leka kudzidalira kuti ndiwe womvetsa zinthu. Kodi maso ako amayang’anitsitsa chuma, pomwe icho sichichedwa kuchoka? Chifukwa ndithu chimadzipangira mapiko ngati a chiwombankhanga n’kuulukira kumwamba.”​—Miyambo 23:4, 5.

ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI KUKHALA WOSANGALALA

MUZIKHALA OKHUTIRA Baibulo limanena kuti: “Pakuti sitinabwere ndi kanthu m’dziko, ndipo sitingatulukemo ndi kanthu. Choncho, pokhala ndi chakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutira ndi zinthu zimenezi.”(1 Timoteyo 6:7, 8) Anthu amene amakhala okhutira ndi zimene ali nazo samangokhalira kudandaula ndipo zimenezi zimawathandiza kuti asamachitire ena nsanje. Komanso chifukwa choti salakalaka zinthu zimene sangazikwanitse, sakhala ndi nkhawa komanso kuvutika maganizo.

MUZIKHALA WOPATSA Baibulo limanena kuti: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Anthu opatsa amasangalala akaona kuti munthu amene amuthandizayo akuonekanso wosangalala. Amamva bwino ngakhale zitakhala kuti sanatayirepo nthawi komanso mphamvu zambiri pothandiza munthuyo. Anthu amene amachita zimenezi amakondedwa, amalemekezedwa komanso amapeza mabwenzi enieni omwe amawachitiranso zinthu mowolowa manja. Zimenezitu ndi zinthu zamtengo wapatali zomwe sitingathe kuzigula ndi ndalama.​—Luka 6:38.

MUZIONA ANTHU ENA KUKHALA OFUNIKA KWAMBIRI KUPOSA KATUNDU Baibulo limanena kuti: “Ndi bwino kudya zamasamba koma pali chikondi, kusiyana ndi kudya nyama ya ng’ombe yamphongo yodyetsedwa bwino pali chidani.” (Miyambo 15:17) Lembali likusonyeza kuti kuchita zinthu limodzi ndi anthu amene mumakondana nawo kumaposa kukhala ndi chuma. Ndipotu chikondi chingatithandize kukhala osangalala monga mmene tionere m’nkhani zotsatira.

Mayi wina wa ku South America, dzina lake Sabina anaona kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo n’kothandiza kwambiri. Mayiyu mwamuna wake anamuthawa ndipo amavutika kulera ana ake aakazi awiri komanso kupeza zinthu zina zofunika. A Sabina amagwira ntchito kumalo awiri ndipo tsiku lililonse amadzuka 4 koloko m’mamawa. Mayiyu amakhala wotanganidwa kwambiri, komabe anaganiza zoyamba kuphunzira Baibulo. Ndiye kodi pano zinthu zikumuyendera bwanji?

Ngakhale kuti amapeza ndalama movutikira, zinthu zinasintha kwambiri pa moyo wake atayamba kuphunzira Baibulo. Panopa a Sabina amaona kuti amasangalala chifukwa chophunzira Mawu a Mulungu. (Mateyu 5:3) Anapeza mabwenzi enieni m’gulu la Yehova ndipo amasangalala akamauza anthu ena zomwe amaphunzira.

Baibulo limanena kuti: “Nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha ntchito zake.” (Mateyu 11:19) Choncho kukhala wokhutira, kukhala wopatsa komanso kuona anthu ena kukhala ofunika kwambiri kuposa zinthu zomwe tili nazo, n’zofunika kwambiri kuti tikhale munthu wosangalala.