Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa Zotani pa Nkhani ya Malungo?

Kodi Mukudziwa Zotani pa Nkhani ya Malungo?

Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linanena kuti m’chaka cha 2013 anthu oposa 198 miliyoni anadwala malungo ndipo anthu pafupifupi 584,000 anamwalira ndi matendawa. Pa anthu 5 alionse, 4 anali ana osakwana zaka 5. Matendawa amapezeka m’mayiko pafupifupi 100 ndipo mwina anthu 3.2 biliyoni akhoza kudwala.

1 ZIZINDIKIRO ZA MALUNGO

Zizindikiro za malungo ndi izi: kutentha thupi, kuzizidwa, kupweteka kwa mutu, kuphwanya thupi, kuchita mseru ndiponso kusanza. Zizindikirozi zikhoza kuonekera pa maola 48 kapena 72 alionse malinga ndi mtundu wa malungo komanso nthawi imene munthu wakhala akudwala.

2 KODI MALUNGO AMAFALIKIRA BWANJI?

  1. Tizilombo ta malungo timalowa m’magazi a munthu akalumidwa ndi udzudzu waukazi wa anofelesi.

  2. Tizilomboti timapita kuchiwindi n’kuyamba kuswana.

  3. Maselo a chiwindi akaphulika tizilomboti timalowa m’maselo ofiira a magazi n’kuswananso mmenemo.

  4. Maselo ofiirawo akaphulika tizilomboto timafalikira m’maselo ena ofiira.

  5. Izi zimachitika mobwerezabwereza. Ndiyeno munthu amamva zizindikiro nthawi iliyonse imene maselo ofiirawo aphulika.

3 KODI TINGADZITETEZE BWANJI?

Ngati mumakhala m’dziko limene kuli malungo, chitani izi:

  • Muzigona m’masikito. Masikitowo azikhala

    • onyikidwa m’mankhwala.

    • osang’ambika.

    • oyalidwa bwino kuti udzudzu usakhale ndi mpata wolowa.

  • Muzipopera mankhwala m’nyumba.

  • Ngati n’kotheka muziika sefa m’mawindo kuti udzudzu usalowe. Mukhozanso kuyatsa fani kuti udzudzu uthawe.

  • Muzivala zovala zoteteza khungu lanu kuti musalumidwe.

  • Pewani malo alionse amene udzudzu ungaswane.

  • Mukayamba kudwala malungo muzipita kuchipatala mwamsanga.

Ngati mukufuna kupita kudziko limene kuli malungo, chitani izi:

  • Fufuzani kaye mfundo zonse zothandiza musananyamuke. Mudziwiretu mtundu wa mankhwala amene angakuthandizeni chifukwa malungo amakhala osiyanasiyana malinga ndi dera. Fufuzaninso zimene muyenera kupewa malinga ndi mmene thupi lanu lilili.

  • Mukafika m’dzikolo, muyenera kutsatira mfundo zimene talemba pamwambapa pa kamutu kakuti, “Ngati mumakhala m’dziko limene kuli malungo.”

  • Mukayamba kudwala malungo pitani kuchipatala mwamsanga. Kumbukirani kuti zizindikiro za malungo zikhoza kuyamba kuonekera patapita mlungu umodzi kapena milungu 4 kuchokera pamene munalumidwa ndi udzudzu.