Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Costa Rica

Dziko la Costa Rica

ZAKA 500 zapitazo, anthu ochokera ku Spain anafika m’dziko la Costa Rica. Anthuwa ndi amene anapatsa dzikoli dzina lakuti Costa Rica poganiza kuti m’derali apezamo golide wambiri. Koma izi si zimene zinachitika. Masiku ano dziko la Costa Rica silimadziwika kuti lili ndi miyala ya mtengo wapatali. Koma limadziwika kuti lili ndi mitengo komanso nyama zambiri zachilengedwe.

Anthu a ku Costa Rica amatchulidwa kuti Atiko. Dzinali linabwera chifukwa choti anthuwa amawonjezera mawu otanthauza ‘chaching’ono’ kapena ‘chochepa’ kumapeto kwa mawu a chinenero chawo. Amakondanso kunena mawu akuti “¡pura vida!” kutanthauza “moyo wabwino.” Amanena mawuwa posonyeza kuyamikira, kuvomereza, podutsana ndi anthu kapena potsanzika.

Nkhalango za ku Costa Rica zili ndi mitengo komanso nyama zosiyanasiyana. Zina mwa nyamazi ndi achule a maso ofiira

Anthu a ku Costa Rica amakonda kudya chakudya chotchedwa gallo pinto. Pokonza chakudyachi, amaphika mpunga ndi nyemba kenako n’kuzisakaniza ndipo amathiramonso zokometsera zina ndi zina. Chakudyachi akhoza kuchidya m’mawa, masana kapena madzulo. Amakondanso kumwa khofi wotchedwa café chorreado. Akamapanga khofiyu, amamusefa pogwiritsa ntchito kansalu komwe amakaika pakathabwa ndipo khofiyo amagwera m’kapu.

M’dziko la Costa Rica muli mipingo ya Mboni za Yehova pafupifupi 450. Misonkhano yawo imachitika m’chinenero chamanja cha komweko, m’Chibiribiri, m’Chikabeka komanso mu zinenero zina 7. Chibiribiri ndi Chikabeka ndi zinenero za nzika za m’dzikoli.

KODI MUKUDZIWA? Ku Costa Rica anapezako miyala yambirimbiri yozungulira ndipo ina ya miyalayi ndi yaikulu kwambiri. Ena amaganiza kuti miyalayi yakhalapo kwa zaka zoposa 1,400. Anthu sadziwa kuti miyalayi ankaigwiritsa ntchito yanji kalelo.

Miyala yozungulira