Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Onetsetsani Mbalame”

“Onetsetsani Mbalame”

MBALAME zimapezeka padziko lonse, ndipo zili m’gulu la zolengedwa zimene anthu amatha kuzidziwa bwino mosavuta. Mbalame zilipo zosiyanasiyana mitundu, kaliridwe komanso zimene zimachita. Izi zimapangitsa kuti anthu azichita chidwi ndi mbalame komanso azisangalala akamaziona.

Tchete

Ngakhale muli panyumba panu, mukhoza kudziwa zambiri zokhudza mbalame inayake chifukwa choona zimene mbalameyo imachita tsiku ndi tsiku. Mwachitsanzo, mungathe kuona njiwa yaimuna ikucheza ndi yaikazi. Mungathenso kuona mbalame zina zikugwira tizilombo touluka, zina zikumanga zisa komanso zina zikudyetsa ana awo. Palinso mbalame zinazake zomwe zimakonda kufukula nyongolotsi.

Nkhanga

Mungathenso kuchita chidwi poona mbalame monga nkhwazi, chiwombankhanga ndi kamtema zikuuluka m’mlengalenga posaka chakudya. Mungachitenso chidwi mutaona mbalame monga mpheta zikukanganirana nyenyeswa za chakudya, njiwa yaimuna itatambasula mapiko pofuna kukopa yaikazi komanso mbalame zinazake zomwe zimauluka m’magulu ndipo zimasokosa kwambiri. Nawonso adokowe ndi atsekwe amachita zodabwitsa kwambiri. Mbalame zimenezi zimatha kusamuka n’kuyenda mtunda wautali kupita kwina. Kwa zaka zambiri anthu akhala akuonetsetsa  mbalamezi kuti adziwe zimene zimachita zikamasamuka. Anthuwa amachita chidwi kuona kuti mbalamezi zikanyamuka zimauluka mtunda wautali n’kukafika kumene zikupitako kenako zimadzabwereranso pa nthawi yake. Ndipotu Mlengi ananena kuti: “Ngakhale dokowe, mbalame youluka m’mlengalenga, imadziwa bwino nthawi yake yoikidwiratu. Ndipo njiwa, namzeze ndi pumbwa, iliyonse mwa mbalame zimenezi imadziwa nyengo yobwerera kumene yachokera.”—Yeremiya 8:7.

Mbalame Zotchulidwa M’Baibulo

Baibulo limatchula mbalame kambirimbiri pofuna kutiphunzitsa mfundo zofunika. Mwachitsanzo, ponena za nthiwatiwa komanso mmene imathamangira, Mulungu anauza Yobu kuti: “Ikatambasula mapiko ake ndi kuwakupiza, imaseka hatchi ndi wokwerapo wake.” * (Yobu 39:13, 18) Mulungu anafunsa Yobu kuti: “Kodi kuzindikira kwako n’kumene kumachititsa kabawi kuuluka pamwamba, . . . kapena kodi lamulo lako n’limene limachititsa chiwombankhanga kuulukira m’mwamba?” (Yobu 39:26, 27) Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa? Tikuphunzira kuti mbalame zimachita zinthu zogometsa kwambiri popanda kuthandizidwa ndi anthufe. Zimene mbalame zimachitazi zimasonyeza kuti Mulungu ndi wanzeru kwambiri.

Mfumu Solomo inalemba za “kulira kwa njiwa” kumene kunkamveka nyengo yachisanu ikamatha. (Nyimbo ya Solomo 2:12) Munthu wina amene analemba nawo buku la Masalimo, ankalakalaka kutumikira panyumba ya Yehova, ndipo ankasirira akaona kuti anamzeze akupezeka panyumbayo nthawi zonse. Iye anati: “Inu Yehova, . . . mbalame zapeza malo okhala pafupi ndi guwa lanu lansembe lalikulu. Namzeze wadzimangira chisa chake pamenepo, ndi kuikamo ana ake!”—Salimo 84:1-3.

“Atate wanu wakumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengo wapatali kuposa mbalame kodi?”—Mateyu 6:26

Nayenso Yesu Khristu anatchula mbalame pophunzitsa mfundo zofunika. Mwachitsanzo palemba la Mateyu 6:26 anati: “Onetsetsani mbalame zam’mlengalenga, pajatu sizifesa mbewu kapena kukolola, kapenanso kusunga chakudya m’nkhokwe. Koma Atate wanu wakumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengo wapatali kuposa mbalame kodi?” Fanizo limeneli limathandiza otsatira a Yesu kudziwa kuti Mulungu amawaona kuti ndi ofunika. Limawathandizanso kudziwa kuti sayenera kumada nkhawa kwambiri kuti apeza bwanji zofunika pa moyo.—Mateyu 6:31-33.

Masiku ano anthu ambiri amakonda kuona mbalame pa nthawi yawo yosangalala. M’pake kuti amachita zimenezi chifukwa pali mbalame za mitundu yosiyanasiyana zomwenso zimachita zinthu zambiri zochititsa chidwi. Anthufe tikhoza kuphunzira zambiri poona zimene mbalame zimachita. Kodi inuyo ‘muzionetsetsa zimene mbalame zimachita?’

^ ndime 6 Nthiwatiwa ndi mbalame yaikulu kwambiri kuposa mbalame zonse ndipo imathamanga mofulumira kwambiri. Mbalameyi imatha kuthamanga mtunda wa makilomita 72 pa ola limodzi osaima.