Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kuvutika Maganizo

Kuvutika Maganizo

Kodi matenda ovutika maganizo ndi otani?

“Ndasokonezeka ndipo ndawerama kwambiri chifukwa cha chisoni changa. Ndayenda uku ndi uku tsiku lonse ndili wachisoni.”—Salimo 38:6.

ZIMENE AKATSWIRI OFUFUZA AMANENA

Aliyense amavutika maganizo nthawi zina koma ngati munthu amangovutika maganizo nthawi zonse n’kumalephera kuchita zinthu zina pa moyo wake, ndiye kuti akudwala matenda ovutika maganizo. Akatswiri amanena zinthu zosiyanasiyana posiyanitsa munthu amene “akuvutika maganizo chifukwa choti wakhumudwa,” ndi munthu amene akudwala “matenda ovutika maganizo.” Koma n’zoona kuti nthawi zina aliyense akhoza kukhumudwa, kudziimba mlandu komanso kudziona kuti ndi wosafunika.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limanena za amuna ndi akazi ambiri amene ankavutika maganizo chifukwa choti akhumudwa. Mwachitsanzo, limanena kuti Hana “anali wokhumudwa kwabasi.” (1 Samueli 1:10) Mawu akuti ‘kukhumudwa kwabasi’ angamasuliridwenso kuti kusweka mtima kapena kuvutika maganizo kwambiri. Pa nthawi ina, Eliya anakhumudwa kwambiri moti anapempha Mulungu kuti achotse moyo wake.—1 Mafumu 19:4.

Nawonso akhristu oyambirira analangizidwa kuti ‘azilankhula molimbikitsa kwa amtima wachisoni.’ (1 Atesalonika 5:14) Mogwirizana ndi zimene buku lina limanena, mawu akuti “amtima wachisoni” amanena za anthu amene “amavutika maganizo kwambiri kwa nthawi yochepa.” Apa zikuonekeratu kuti nawonso anthu amene amatchulidwa m’Baibulo ankavutika maganizo.

 Kodi munthu amavutika maganizo chifukwa chakuti walakwitsa chinachake?

“Pakuti tikudziwa kuti chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zowawa mpaka pano.”—Aroma 8:22.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limanena kuti anthu amadwala chifukwa chakuti makolo athu oyambirira anasankha dala kusamvera Mulungu. Mwachitsanzo, lemba la Salimo 51:5 limati: “Anandilandira mu zowawa za pobereka ndili wochimwa. Ndipo ndine wochimwa kuchokera pamene mayi anga anatenga pakati panga.” Ndipo lemba la Aroma 5:12 limati: ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’ Chifukwa chakuti tinatengera uchimo kwa Adamu, tonsefe timadwala komanso kuvutika maganizo. Baibulo limanena kuti chifukwa cha uchimo umenewu, “chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zowawa mpaka pano.” (Aroma 8:22) Komabe, Baibulo limatipatsanso chiyembekezo, chomwe dokotala aliyense sangapereke. M’Baibulo muli lonjezo la dziko latsopano lamtendere mmene simudzakhala matenda kapena kuvutika maganizo.—Chivumbulutso 21:4.

Kodi mungatani ngati mumavutika maganizo?

“Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”—Salimo 34:18.

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Pali zinthu zina zomwe simungathe kuzisintha ndipo nthawi zina zinthu zoipa zingakuchitikireni. (Mlaliki 9:11, 12) Koma pali zinthu zina zomwe mungachite kuti musamavutike maganizo kwambiri zinthu zoipa zikakuchitikirani.

ZIMEME BAIBULO LIMANENA

Baibulo limanena kuti odwala amafunika dokotala. (Luka 5:31) Choncho ngati mukuvutika maganizo kwambiri, palibe cholakwika chilichonse ndi kukaonana ndi adokotala. Komanso Baibulo limasonyeza kuti pemphero ndi lofunika kwambiri. Mwachitsanzo, lemba la Salimo 55:22 limati: “Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza. Sadzalola kuti wolungama agwedezeke.” Mukamapemphera mumakhala kuti mukulankhulana ndi Yehova Mulungu, yemwe amakhala “pafupi ndi anthu a mtima wosweka.”—Salimo 34:18.

Mungachitenso bwino kuuzako mnzanu za vuto limeneli. (Miyambo 17:17) Mtsikana wina yemwe ndi wa Mboni za Yehova, dzina lake Daniela, ananena kuti: “Mnzanga yemwenso ndi wa Mboni, anakhala akundilimbikitsa kuti ndizimuuza mmene ndikumvera ndikamavutika maganizo. Ngakhale kuti zaka za m’mbuyomu sindinkafuna kuti ndizilankhulana ndi aliyense za nkhani imeneyi, ndinazindikira kuti ndi zimene ndinkafunika kuchita nthawi yonseyi. Ndinadabwa kwambiri kuti ndinamva kupepuka mumtima nditamuuza mmene ndinkamvera.”