Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzikhala ndi Okuthandizani

Muzikhala ndi Okuthandizani

Kukhala ndi anthu amene angamakulangizeni komanso kukuthandizani n’kofunika pamene muli pa sukulu komanso mukadzamaliza sukulu.

KODI ndani amene angakuthandizeni kuti zinthu zizikuyenderani bwino ku sukulu?

Anthu am’banja mwanu.

Mtsikana wina wazaka 18, wa ku Brazil, dzina lake Bruna, ananena kuti: “Homuweki ikakhala kuti yandivuta, bambo anga ankandifotokozera bwino kenako n’kundifunsa mafunso. Koma sankandiuzira mayankho chifukwa ankafuna kuti ndipeze ndekha.” *

Mfundo yothandiza: Funsani makolo anu kuti anene mmene ankakhozera phunziro limene limakuvutanilo. Ngati ankakhoza bwino, ndiye kuti angakuthandizeni.

Aphunzitsi.

Aphunzitsi ambiri amasangalala akaona kuti mwana wasukulu akufunitsitsa kuti azikhoza bwino ndipo amayesetsa kuti amuthandize.

Mfundo yothandiza: Mungachite bwino kuwauza aphunzitsi anu kuti: “Ndimafuna nditamakhoza bwino phunziroli koma limandivuta. Kodi mungandithandize bwanji?”

Anthu ena okuthandizani.

Mwina munthu wina amene mumamudalira akhoza kukuthandizani. Zimenezi zingakuthandizeni m’njira ziwiri izi: Choyamba, mungapeze thandizo limene mukufuna ndipo chachiwiri, mungaphunzire kudalira anthu ena, zomwenso zingadzakuthandizeni mukadzakula. Dziwani kuti munthu aliyense zimamuyendera bwino ngati anthu ena amuthandiza.​—Miyambo 15:22.

Mfundo yothandiza: Afunseni makolo anu kuti akuuzeni anthu ena amene iwo akuganiza kuti akhoza kukuthandizani.

Mfundo yofunika kuikumbukira: Palibe cholakwika ndi kupempha ena kuti akuthandizeni.

Yambani kutsatira malangizo amenewa. Lembani mayina a anthu awiri kapena atatu amene ndi zitsanzo zabwino ndipo mumafuna mutatengera chitsanzo chawo. Mwina mmodzi wa anthu amenewa akhoza kukuthandizani pa nkhani ya sukulu.

^ ndime 4 Ngati muli ndi m’bale wanu wamkulu akhozanso kukuthandizani.