Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Batik—Nsalu Zokongola za ku Indonesia

Batik—Nsalu Zokongola za ku Indonesia

Batik​Nsalu Zokongola za ku Indonesia

KU Indonesia kuli nsalu zokongola kwambiri zotchedwa Batik. Nsaluzi zinayamba kupangidwa kale kwambiri, ndipo zidakapangidwabe mpaka pano moti anthu olemera komanso anthu wamba amazikonda kwambiri. Nsaluzi ndi zamitundu yosiyanasiyana komanso amazipanga mosiyanasiyana. Koma kodi nsalu za Batik zimapangidwa bwanji? Nanga anayamba kupanga nsaluzi ndani? Kodi anthu amazigwiritsira ntchito bwanji masiku ano?

Anthu anayamba kupanga nsalu ya Batik kuyambira kale kwambiri ndipo amazipanga m’njira yoti utoto umene ajambulira maluwa ake usasuluke. Nsaluzi ndi mbali ya chikhalidwe cha anthu a ku Indonesia, komabe zimapezekanso m’mayiko ena padziko lonse.

Kodi Zimapangidwa Bwanji?

Popanga nsaluzi amatenga kachipangizo kachitsulo komwe mkati mwake amathiramo phula la madzimadzi. Akatero amagwiritsa ntchito kachipangizoka kujambulira maluwa kapena mizera yokongola pansaluyo. Zojambulazo zikauma, nsaluyo amaidaya ndi utoto. Utotowo susintha mtundu wa phula limene ajambulira lija. Akatero amatha kuviika nsaluyo mu utoto wa mitundu yosiyanasiyana kuti ikongole.

M’zaka za m’ma 1800, akatswiri opanga nsalu za Batik anayamba kugwiritsa ntchito zodindira zachitsulo popaka phula pansaluzo. Njira imeneyi inali yofulumilirapo poyerekeza ndi kujambula pamanja ndipo inkawathandiza kuti apange nsalu zambiri koma zofanana. Koma pofika m’zaka za m’ma 1900, makampani anayamba kugwiritsa ntchito makina apamwamba kujambulira maluwa pansaluzi. Masiku ano nsalu za Batik zopangidwa pa manja zimapezekabe, koma zopangidwa m’mafakitale ndi zimene zikupezeka kwambiri.

Nthawi zambiri nsalu za Batik zimakhala za thonje kapena silika. Utoto umene amadayira nsaluzi amaupanga ndi zinthu monga masamba, mitengo, makungwa a mitengo komanso zinthu zina zokometsera zakudya. Nthawi zina amagwiritsanso ntchito utoto wopangidwa kufakitale. Poyamba penipeni akafuna kujambula maluwa kapena mizera pansaluzi, ankagwiritsa ntchito masamba osinja, mafuta anyama kapena matope m’malo mwa phula. Masiku ano amagwiritsa ntchito phula lopangidwa ku fakitale, koma anthu ena amagwiritsabe ntchito phula limene amalipanga okha posakaniza parafini ndi phula la njuchi.

Kodi Zinayamba Kupangidwa Liti?

Palibe amene amadziwa nthawi komanso malo enieni amene nsalu za Batik zinayamba kupangidwira. Ku China kuli nsalu zina za Batik zopangidwa m’zaka za m’ma 500 C.E. Palibe amene amadziwa bwinobwino nthawi imene anayamba kupanga nsaluzi ku Indonesia, koma zikuoneka kuti pofika m’ma 1600, anthu a ku Indonesia anali akuchita malonda a nsalu zimenezi.

M’zaka zapitazi, nsalu za Batik zatchuka kwambiri ku Indonesia ndipo zafika pokhala chizindikiro cha dzikoli. M’chaka cha 2009, bungwe la UNESCO linaika nsalu za Batik pa mndandanda wa “Zinthu Zakale Zothandiza Kusunga Chikhalidwe” cha dziko la Indonesia. Bungweli linachita zimenezi pofuna kusonyeza mmene anthu a ku Indonesia agwiritsira ntchito nsaluzi kwa nthawi yaitali komanso mmene zakhudzira chikhalidwe chawo.

Kutchena Zovala za Batik

Pali njira zosiyanasiyana zopangira komanso zovalira nsalu za Batik mogwirizana ndi zimene anthu amakhulupilira. Anthu a m’chigawo chilichonse ku Indonesia ali ndi mtundu komanso kapangidwe kawokawo ka nsaluzi. Mwachitsanzo, anthu a kumpoto kwa chilumba cha Java m’dzikolo amakonda kuvala nsalu za Batik zowala kwambiri, zojambulidwa maluwa, mbalame ndi nyama zina. Pomwe anthu a pakati pa chilumbachi amakonda kuvala nsalu zosawala kwambiri ndipo zimakhala zojambulidwa mizeramizera. Pali mitundu 3,000 ya kajambulidwe ka maluwa kapena mizera pansalu za Batik yodziwika bwino.

Nthawi zambiri azimayi amakonda kukolekera nsalu paphewa. Nsalu imeneyi amaitchula kuti selendang ndipo nthawi zina amaberekera mwana kapena kunyamulirapo zinthu zimene agula kumsika. Komanso kukatentha amagwiritsa ntchito nsaluyi ngati duku.

Azibambo amakonda kuvala kachipewa kamene amakatchula ku iket kepala. Popanga kachipewaka amatenga nsaluyi n’kuikulunga kumutu ndipo imaoneka ngati nduwira. Azibambo amakonda kuvala zovala za nsalu imeneyi pakakhala zochitika zapadera.

Nsalu za Batik amapangiranso chitenje chomwe amachitchula kuti sarong. Nthawi zina chitenjechi amachisoka kuti chikhale ngati siketi ndipo chimavalidwa ndi azimayi ndi azibambo omwe.

Nsalu za Batik amasokera zinthu zosiyanasiyana monga matharauza komanso zovala zapamwamba kwambiri. Komanso amatha kuzigwiritsa ntchito ngati zopachika m’makoma, nsalu zapatebulo, zoyala pabedi komanso ngati nsalu zojambulapo zinthu zosiyanasiyana. Anthu okaona malo m’dziko la Indonesia amati akapita kumsika amatha kupeza zinthu zosiyanasiyana zopangidwa kuchokera ku nsaluzi, monga zikwama, masandasi, zotchingira magetsi komanso nsalu zophimbira makompyuta. Nsalu za Batik zimagwiritsidwa ntchito m’njira zosiyanasiyana. Kunena zoona nsaluzi ndi zokongola komanso zochititsa chidwi.

[Chithunzi patsamba 23]

Kachipangizo kachitsulo komwe amathiramo phula ndipo amakagwiritsa ntchito pojambulira maluwa ndi mizera yokongola kwambiri pansalu za Batik

[Chithunzi patsamba 23]

Nsaluyi akaipaka phula amaidaya poiviika mu utoto mobwerezabwereza

[Zithunzi patsamba 23]

Zovala za Batik

1. Selendang

2. Iket kepala

3. Sarong