Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Mukakhala ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?

Kodi Mungatani Mukakhala ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?

Kodi Mungatani Mukakhala ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?

CHAKA ndi chaka anthu ambiri padziko lonse amakhala ndi maganizo ofuna kudzipha. Baibulo limanena chifukwa chimene anthu amakhalira ndi nkhawa mpaka kufika pofuna kudzipha. Limanena kuti tikukhala ‘m’nthawi yovuta,’ ndipo pa chifukwa chimenechi anthu akukumana ndi mavuto ambiri. (2 Timoteyo 3:1; Mlaliki 7:7) Munthu akamakumana ndi mavuto aakulu, angaganize zongodzipha kuti athane ndi mavutowo. Kodi mungatani ngati muli ndi maganizo amenewa?

Dziwani Kuti Siinu Nokha

Ngakhale kuti mungamaone kuti mavuto amene mukukumana nawo ndi osapiririka, muzikumbukira kuti siinu nokha amene mukukumana ndi mavuto komanso pafupifupi aliyense akulimbana ndi vuto linalake. Baibulo limanena kuti: “Chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zowawa mpaka pano.” (Aroma 8:22) Ngakhale kuti panopa mungamaone kuti mavuto anuwo sadzatha, zoona zake n’zakuti zinthu zimasintha pakapita nthawi. Ndiyeno kodi panopa muyenera kuchita chiyani?

Uzani Mnzanu Wodalirika Mavuto Amene Mukukumana Nawo. Baibulo limanena kuti: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo ilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.” (Miyambo 17:17) Baibulo limasonyeza kuti Yobu, yemwe anali munthu wokhulupirika, ankafotokozera anzake mavuto ake. Pa nthawi yomwe ‘ankanyansidwa ndi moyo wake,’ iye ananena kuti: “Ndilankhula mwamphamvu za nkhawa zanga. Ndilankhula chifukwa cha kuwawa kwa moyo wanga.” (Yobu 10:1) Mukauzako anthu ena za mavuto anu, mumamvako bwino mumtima ndipo zingakuthandizeni kuti muyambe kuona mavuto anuwo mwanjira ina.

Pempherani kwa Yehova. Anthu ena amaganiza kuti pemphero limangothandiza anthu kuti azingomvako bwino pang’ono, koma Baibulo limafotokoza zosiyana ndi zimenezo. Lemba la Salimo 65:2 limati Yehova Mulungu ndi “Wakumva pemphero” komanso lemba la 1 Petulo 5:7 limati: “Amakuderani nkhawa.” Baibulo limanena mobwerezabwereza za kufunika kodalira Mulungu. Taonani malemba otsatirawa:

“Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukira m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.”—MIYAMBO 3:5, 6.

“Anthu amene amamuopa [Yehova] adzawachitira zokhumba zawo, adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipo adzawapulumutsa.”—SALIMO 145:19.

“Ifetu timamudalira kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.”—1 YOHANE 5:14.

“Yehova amakhala kutali ndi anthu oipa, koma amamva pemphero la anthu olungama.”—MIYAMBO 15:29.

Mukamauza Mulungu mavuto amene mukukumana nawo, iye adzakuthandizani. N’chifukwa chake Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Mukhulupirireni nthawi zonse, . . . Mukhuthulireni za mumtima mwanu.”—Salimo 62:8.

Ngati Pali Vuto Lalikulu

Kafukufuku amasonyeza kuti anthu ambiri amene amadzipha amakhala kuti anali ndi vuto lovutika maganizo. * Zimenezi zikusonyeza kuti ngati muli ndi maganizo ofuna kudzipha, ndibwino kupita kuchipatala kuti akakuthandizeni. Dokotala angakupatseni mankhwala kapena malangizo okhudza zakudya zoyenera. Nthawi zina kuchita masewera olimbitsa thupi kumathandiza kwambiri. Anthu ambiri amavomereza kuti kupita ku chipatala ndi kothandiza kwambiri. *

M’Baibulo muli mfundo zambiri zomwe zingakuthandizeni komanso kukulimbikitsani. Mwachitsanzo, lemba la Chivumbulutso 21:4 limanena kuti Yehova Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.” Mulungu ndi amene akulonjeza zimenezi ndipo kuganizira mozama za lonjezo limeneli kungatithandize kupirira mavuto.

Mboni za Yehova zikuuza anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse uthenga wa m’Baibulo wolimbikitsa umenewu. Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri ali ndi chiyembekezo chakuti m’tsogolomu mavuto a anthu adzatha. Kuti mudziwe zambiri, funsani Mboni za Yehova za m’dera lanu. Mungachite zimenezi popita ku Nyumba ya Ufumu kapena polemba kalata ku adiresi yoyenerera pa maadiresi amene ali patsamba 5 la magazini ino. Kapenanso mungapite pa malo athu a pa Intaneti pogwiritsa ntchito adiresi iyi: www.isa4310.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Ngati mukufuna kudziwa zambiri pa nkhaniyi, onani Galamukani! ya July 2009 tsamba 3 mpaka 9.

^ ndime 13 Galamukani! sisankhira anthu mankhwala. Aliyense ali ndi udindo wofufuza bwinobwino za chithandizo cha mankhwala amene akufuna kulandira.

[Bokosi patsamba 16]

BAIBULO LINGAKUTHANDIZENI

● “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.”—Afilipi 4:6, 7.

● “Ndinafunsa kwa Yehova ndipo iye anandiyankha, pakuthawathawa kwanga konse iye anandilanditsa.”—Salimo 34:4.

● “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”—Salimo 34:18.

● “Iye amachiritsa anthu osweka mtima, ndipo amamanga zilonda zawo zopweteka.”—Salimo 147:3.

[Bokosi pamasamba 17, 18]

NGATI MULI NDI MAGANIZO OFUNA KUDZIPHA . . .

Uzani mnzanu wodalirika mavuto amene mukukumana nawo

Pempherani kwa Yehova

Pitani kuchipatala

[Bokosi/Chithunzi patsamba 18]

ZIMENE ACHIBALE NDI ANZAKE ANGACHITE

Nthawi zambiri munthu akafuna kudzipha, achibale komanso anzake apamtima ndi amene amakhala oyambirira kudziwa. Choncho, ngati mwazindikira zimenezi ndi bwino kuchitapo kanthu mwansanga. Pamene akukufotokozerani mavuto ake, muyenera kumumvetsera moleza mtima. Musapeputse mavuto amene munthuyo akukumana nawo. Baibulo limanena kuti: “Lankhulani molimbikitsa kwa amtima wachisoni.” (1 Atesalonika 5:14) Limbikitsani munthu amene akuvutika maganizoyo kuti alandire chithandizo ndipo onetsetsani kuti walandiradi chithandizocho.