Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chigoba cha Nkhono Yam’madzi

Chigoba cha Nkhono Yam’madzi

Kodi Zinangochitika Zokha?

Chigoba cha Nkhono Yam’madzi

● Nkhono inayake imene imapezeka pansi pa nyanja ya Indian ili ndi chigoba cholimba kwambiri kuposa chigoba cha nyama ina iliyonse. Chigobachi chimathandiza kuti nkhonoyi izitha kukhala pansi kwambiri pa madzi, mwina pakuya mamita 2,400. Chigobachi chimathandizanso kuti nkhonoyi izitha kukhala m’madzi a asidi wambiri komanso otentha kwambiri. Nkhonoyi imatha kukhala bwinobwino ngakhale pamalo pamene pamatuluka madzi otentha kwambiri ochokera pansi pa nthaka. Chigobachi chimatetezanso nkhonoyi kuti isadyedwe ndi nyama zina.

Taganizirani izi: Chigoba cha nkhonoyi chili ndi mbali zitatu. Mbali yakunja ya chigobachi inapangidwa ndi aironi. Mbali yapakati inapangidwa ndi mapulotini ofanana ndi a zigoba za nkhono zina. Ndipo mbali yamkati inapangidwa ndi kasiyamu. Mbali zitatu zimenezi zimachititsa kuti chigobachi chikhale cholimba kwambiri ndipo zimenezi zimateteza nkhonoyi, chifukwa nyama zina zimalephera kuchiphwanya. Mwachitsanzo nkhanu zinazake zikuluzikulu zimapana chigoba cha nkhonoyi kwa masiku ambiri koma zimalephera kuchiswa.

Magazini ya Discover inanena kuti akatswiri apeza kuti “mbali yakunja ya chigobachi inapangidwa kuti ikamasweka, mphamvu zomwe zikuswa chigobacho zisamapite patali.” Akatswiriwo ataswa chigobacho ndi chida cholimba kwambiri chopangidwa ndi diamondi, anapeza kuti “mbali yakunja yokha ya chigobacho ndi imene inkang’aluka komanso timing’alu take tinali tating’onoting’ono kwambiri.” Pamene chigobacho chikuswedwa, mbali yapakati ija imakhala ikuchepetsa mphamvuzo kuti zisalowerere mkati mwa chigobacho.

Potengera chigoba cha nkhonoyi, akatswiri akuganizira zopanga zipewa zolimba kwambiri, zovala zosalowa chipolopolo, komanso zitsulo zopangira sitima ndi ndege. Magazini ya Discover inanenanso kuti “ngati atapanga mapaipi onyamula mafuta m’nyanja ya Arctic potengera chigoba chimenechi, mapaipi ake sangamaphulike akamenyedwa ndi madzi oundana.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti nkhonoyi ikhale ndi chigoba cholimba chonchi, kapena ndi umboni wakuti inachita kulengedwa?

[Chithunzi patsamba 23]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Chida cholimba kwambiri

Mbali yakunja

Mbali yapakati

Mbali yamkati

[Mawu a Chithunzi patsamba 23]

Courtesy Anders Warén