Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Ndani Ankagwira Ntchito Imeneyi?

Kodi ndi atsogoleri awiri ati a fuko la Isiraeli omwe anali abusa? Lembani mayankho anu m’mizere yomwe ili munsiyi.

1. ZOKUTHANDIZANI: Werengani Eksodo 3:1.

․․․․․

2. ZOKUTHANDIZANI: Werengani 1 Samueli 17:34-36.

․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi mbusa wabwino ankafunika kusonyeza makhalidwe otani? Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anadziyerekezera ndi mbusa pamene ophunzira ake anawayerekezera ndi nkhosa?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Yohane 10:11-16.

KODI MUKUDZIWA CHIYANI ZOKHUDZA MFUMU ASA?

3. Kodi Asa anatani atangokhala mfumu?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 2 Mbiri 14:2-5.

․․․․․

4. Kodi ankhondo zikwi chikwi chimodzi amene anabwera kudzamenyana ndi Asa anali ochokera dziko liti?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 2 Mbiri 14:9, 10.

․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi Asa anatani atapatsidwa uphungu ndi Hanani?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 2 Mbiri 16:7-10.

Kodi zimene Asa anachita zinali zabwino? Kodi mukapatsidwa uphungu muyenera kutani, ndipo n’chifukwa chiyani muyenera kuchita choncho?

ZITHUNZI ZOTI ANA APEZE

Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse?

KUCHOKERA M’MAGAZINI INO

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.

TSAMBA 20 Kodi dziko lonse lili m’manja mwa ndani? 1 Yohane 5:․․․

TSAMBA 21 Kodi chikondi sichingakuchititseni chiyani? Aroma 13:․․․

TSAMBA 26 Kodi tiyenera kupewa chiyani? 1 Atesalonika 4:․․․

TSAMBA 26 Kodi amene amachita dama amachimwira chiyani? 1 Akorinto 6:․․․

● Mayankho ali patsamba 22

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31

1. Mose.

2. Davide.

3. Anachotsa kulambira konyenga.

4. Itiyopiya.