Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mphamvu Zimene Zimateteza Dziko

Mphamvu Zimene Zimateteza Dziko

Mphamvu Zimene Zimateteza Dziko

MUMLENGALENGA muli cheza choopsa ndiponso zimiyala zikuluzikulu zomwe zimakhala zikuyendayenda. Koma dziko lathu limazungulira bwinobwino popanda kuwombana ndi zinthu zimenezi. Kodi zimatheka bwanji? N’chifukwa chakuti pali mphamvu zimene zimateteza dzikoli. Ndipo dzikoli lili ndi nyesi imene imakankha zinthu zimenezi kuti zisagwere padzikoli.

Nyesi ya dzikoli imachokera pansi penipeni pa nthaka ndipo imafika mpaka mlengalenga (monga mukuonera pa chithunzi cha kumanjaku). Nyesi imeneyi imathandiza kuti cheza choopsa komanso zinthu zina zoopsa zochokera ku dzuwa zisafike padziko pano. Zina mwa zinthu zimene zimachokera ku dzuwa ndi monga mphepo yotentha kwambiri ndiponso moto wothovoka mwamphamvu. Zinthu zimenezi ndi zoposa mabomba mabiliyoni ambirimbiri ophulika nthawi imodzi. Zinthu zonsezi zimachititsa kuti nthawi zina kumpoto kwenikweni komanso kum’mwera kwenikweni kwa dzikoli kuzioneka waliwali.

Mumlengalenga mumateteza dzikoli m’njira inanso. Muli mpweya wina wofanana ndi mpweya umene timapuma, womwe umathandiza kuti cheza choopsa chochokera kudzuwa chisafike padzikoli. Zimenezi zimathandiza kuti anthu ndi zamoyo zina zisawonongeke padzikoli. Chochititsa chidwi ndi chakuti kuchuluka kwa mpweyawu m’mlengalengamo kumasinthasintha malinga ndi kuchuluka kwa cheza chimene chikubwera kuchokera kudzuwa. Izi zimathandiza kwambiri kuteteza dzikoli.

Komanso chifukwa cha mlengalenga, tsiku lililonse dzikoli limatetezedwa kuti lisawombedwe ndi miyala imenenso imayenda mozungulira dzuwa. Ina mwa miyala imeneyi imakhala ikuluikulu kwambiri. Koma n’zosangalatsa kuti yambiri imaphulika m’mlengalenga momwemo n’kumaoneka ngati nyenyezi zothothoka.

Komatu pali cheza china chofunika pa zamoyo chomwe chimadutsa bwinobwino m’mlengalenga n’kufika padzikoli. Cheza chimenechi chimathandiza kuti padziko pano pazikhala powala ndiponso potenthera bwino. Mumlengalenga mumathandizanso kuti kutentha kufike mbali zonse za dzikoli. Ndipo kukada mumlengalenga mumakhala ngati bulangete lothandiza kuti dziko lisazizire kwambiri.

Zonsezitu n’zodabwitsa ndipo mpaka pano anthu sazimvetsa bwinobwino. Chinthu chinanso chovuta kumvetsa ndicho kuchuluka kwa madzi padzikoli.