Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Gulugufe Amadziwira Komwe Akupita

Mmene Gulugufe Amadziwira Komwe Akupita

Panagona Luso

Mmene Gulugufe Amadziwira Komwe Akupita

▪ Mtundu winawake wa agulugufe umauluka makilomita 3,000 kuchoka ku Canada kupita ku nkhalango ina yaing’ono ya ku Mexico. Komatu agulugufe amenewa ali ndi ubongo waung’ono ngati kanjere kampiru. Kodi amadziwa bwanji komwe akupita?

Taganizirani Izi: Agulugufe amenewa amadziwa komwe akupita poona pomwe pali dzuwa. Koma palinso zina zimene zimawathandiza. Agulugufe amenewa mwachibadwa amadziwa nthawi ndi zomwe angachite malinga ndi kayendedwe ka dzuwa. Dokotala wa mitsempha, Steven Reppert, ananena kuti mtundu umenewu wa agulugufe “uli ndi luso lapadera kwambiri lochita zinthu potsatira nthawi kuposa tizilombo ndiponso nyama zina zomwe zafufuzidwapo.”

Kuphunzira zambiri za mmene agulugufe amenewa amadziwira nthawi kungathandize asayansi kudziwa zochuluka za mmene anthu ndi nyama amadziwira nthawi mwachibadwa. Zingathandizenso kupeza mankhwala atsopano a matenda a mitsempha. Reppert anapitiriza kuti: “Ndikufuna kudziwa mmene ubongo umadziwira nthawi ndi koyenera kupita ndipo agulugufe amenewa ndi chitsanzo chabwino kwambiri pankhani imeneyi.”

Kodi Mukuganiza bwanji? Kodi luso limene agulugufe amenewa ali nalo lotha kudziwa kumene akupita anangokhala nalo mwangozi kapena ndi umboni wakuti analengedwa ndi Mlengi waluso?

[Chithunzi/Mapu patsamba 10]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Agulugufe awa amauluka makilomita 3,000 kuchoka ku Canada kupita ku nkhalango yaing’ono ya ku Mexico

[Mapu]

CANADA

UNITED STATES OF AMERICA

MEXICO

MEXICO CITY

[Mawu a Chithunzi patsamba 10]

Background: © Fritz Poelking/age fotostock