Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Imfa Ndi Mapeto a Zonse?

Kodi Imfa Ndi Mapeto a Zonse?

Kodi Imfa Ndi Mapeto a Zonse?

MU February 1987, bambo wina wazaka 85 anasiya kugwiritsa ntchito makina othandiza impso zake kugwira bwino ntchito. Makina amenewa ankamuthandiza kukhala ndi moyo. Patapita milungu iwiri, bamboyu anamwalira kunyumba kwake, mwana wake wamwamuna yekhayo akuona.

Nthawi yomaliza imene bamboyu anali limodzi ndi mwana wake imeneyi, inawapatsa mpata wokambirana nkhani imene anali atakambiranapo kale, yakuti: Kodi n’zotheka kuti amene ali kumanda adzakhalenso ndi moyo? Bamboyu, yemwe anali wophunzira kwambiri, ankakayikira. Iye ankakayikira chifukwa chakuti ankakhulupirira mfundo yakuti zamoyo zinakhalako mwa kuchita kusanduka komanso anali kudana ndi chipembedzo chifukwa cha chinyengo chake. Iye ankati amakhulupirira kuti n’zosatheka kudziwa ngati kuli Mulungu kapena ayi.

Pofuna kutonthoza bambo akewo ndi kuwapatsa chiyembekezo, mwanayo anawafotokozera kuti n’zotheka kuti amene ali kumanda adzakhalenso ndi moyo. Ali pafupi kumwalira, bambowo anavomereza kuti angakonde kudzakhalanso ndi moyo wamphamvu ndi wathanzi.

Tiyenera Kulimba Mtima Tikamaganizira za Imfa

Anthu ambiri mwinanso onse atapatsidwa mwayi, angakonde kudzakhalanso ndi moyo wamphamvu ndi wathanzi m’dziko lamtendere. Anthu sali ngati nyama, zimene Baibulo limanena kuti ndi “zopanda nzeru,” kapena kuti siziganiza. (2 Petulo 2:12) Anthufe timaika maliro ndipo timaganiza za m’tsogolo. Sitifuna kukalamba, kudwala ndiponso kufa. Komatu izi ndi zimene zimachitika.

Tikaganiza kuti tsiku lina ifeyo kapena wina amene timam’konda adzafa, timamva chisoni kwambiri ndipo timachita mantha. Komabe Baibulo limatilimbikitsa kuti sitiyenera kuchita mantha tikamaganiza za imfa. Ilo limati: “Kunka ku nyumba ya maliro kupambana kunka ku nyumba ya madyerero.” Ndipo limanenanso kuti: “Omwe ali ndi moyo adzakumbukirapo.” (Mlaliki 7:2) N’chifukwa chiyani tiyenera kukumbukira kapena kuganizira kwambiri za imfa?

Chifukwa chake n’chakuti, mwachibadwa timafuna kukhala ndi moyo komanso kusangalala ndi moyowo m’dziko lamtendere ndi lachitetezo. Palibe amene amafuna kufa. N’zovuta, mwinanso n’zosatheka, kuvomereza kuti tsiku lina tidzafa. Baibulo limanena chifukwa chake, kuti: “[Mulungu] waika umuyaya m’maganizo mwa anthu,” kapena kuti “m’mitima yawo.” (Mlaliki 3:11, Revised Standard Version) Ife timafuna kukhala ndi moyo, osati kufa. Ndiyeno taganizirani: Kodi maganizo amenewa akanakhala amphamvu kwambiri chonchi kukanakhala kuti sichinali cholinga cha Mlengi wathu kuti tikhale ndi moyo wosatha? Kodi munthu atamwalira, n’zotheka kudzakhalanso ndi moyo wathanzi, wosangalatsa ndi wopanda mapeto?

Chifukwa Chokhulupirira Zimenezi

Chaka chatha, m’magazini ina yofalitsidwa ndi bungwe la anthu opuma pa ntchito la American Association of Retired Persons, munali nkhani yakuti “Munthu Akafa Amakhalanso ndi Moyo.” Atafunsa anthu ambiri azaka zoposa 50, anapeza kuti “pafupifupi anthu atatu mwa anthu anayi alionse (73 peresenti) ananena kuti: ‘Ndimakhulupirira kuti munthu akafa amakhalanso ndi moyo.’” (AARP The Magazine) Komabe magaziniyi inanenanso kuti pafupifupi munthu mmodzi mwa anthu anayi alionse ananena kuti: “Ndimakhulupirira kuti ndikafa, basi ndi mapeto a zonse.” Koma kodi zimenezi ndi zimene anthu amafunadi kukhulupirira?

M’nkhani yomweyo, Tom, Mkatolika wa ku New York, ananena kuti: “Mukudziwa, abusa amaphunzitsa kuti munthu akafa amakhalanso ndi moyo. Ine ndimaona kuti anthu amaphunzitsa zosiyanasiyana pa nkhaniyi. Zili kwa iwe kusankha zimene ukufuna kukhulupirira. Ine ndimapita ku Misa. Zochita zanga zimasonyeza ngati kuti ndimakhulupirira kuti munthu akafa amakhalanso ndi moyo, koma sindikhulupirira. Ngati ndi zoona kuti amakhalanso ndi moyo, basi ndiye kuti ndi mwayi.”

Mofanana ndi Tom, ambiri amakayikira. Mwachitsanzo, bambo amene tamutchula poyamba uja nthawi zina ankauza mwana wake kuti: “Kukhulupirira za chipembedzo ndi kwabwino kwa anthu amene amaopa imfa.” Komatu kukhulupirira kuti kuli Mlengi wamphamvuyonse kumathandiza munthu kupeza mayankho a zinthu zovuta kwambiri kuzimvetsa. Ndipo bamboyo anafika povomereza mfundo imeneyi. Anthu enanso okayikira akakamizika kuvomereza.

Mwachitsanzo, pakangodutsa milungu itatu mayi atatenga pathupi, maselo a ubongo amayamba kupangika. Maselo amenewa amawonjezereka mofulumira kwambiri, ndipo nthawi zina amafika 250,000 pa mphindi imodzi. Pakatha miyezi 9, mwana amabadwa ali ndi ubongo wamphamvu zodabwitsa, wotha kuphunzira. Katswiri wa sayansi ya zamoyo, James Watson, ananena kuti: “Pa zinthu zonse zimene tatulukira m’chilengedwechi, sitinatulukirepo chinthu chovuta kumvetsa ngati ubongo wa munthu.”

Anthu ambiri akaganizira zozizwitsa ngati zimenezi, amagoma. Nanga bwanji inuyo? Kodi kuganizira zimenezi kwakuthandizani kupeza yankho la funso limene munthu wina anafunsa kalekalelo lakuti: “Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?” Kenako munthuyo anayankha Mulungu motsimikiza kuti: “Inu mudzaitana ndipo ine ndidzayankha. Mudzalakalaka ntchito ya manja anu.”—Yobu 14:14, 15, NW.

Zoonadi, tingachite bwino kukambirana umboni wotipangitsa kukhulupirira kuti munthu akafa adzakhalanso ndi moyo.