Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Munthu Wosangalala Kodi Amakhaladi ndi Thanzi Labwino?

Munthu Wosangalala Kodi Amakhaladi ndi Thanzi Labwino?

Munthu Wosangalala Kodi Amakhaladi ndi Thanzi Labwino?

“Mtima wosekerera uchiritsa bwino.” Mawu amenewa analembedwa ndi mfumu yanzeru ya Isiraeli zaka 3000 zapitazo. (Miyambo 17:22) Masiku ano madokotala azindikira kuti mawu amenewa ndi oona. Koma kwa anthu ambiri sizophweka kukhala ndi “mtima wosekerera.”

Ambirife timalephera kupewa mavuto a tsiku ndi tsiku ndipo zimenezi zimachititsa kuti tikhale okhumudwa ndi osasangalala. Koma kafukufuku waposachedwapa wasonyeza kuti kukhala wosangalala n’kothandiza ngakhale kuti n’kovuta.

Kukhala wosangalala kukutanthauza “kusataya mtima; kukhala ndi chidaliro kuti zinthu ziyenda bwino.” Kodi munthu wosangalala akalephera kuchita chinachake, amatani? Saona kuti iye ndi wolephera. Izi sizitanthauza kuti iye savomereza zimene zachitikazo. M’malo mwake, amaiona nkhaniyo bwinobwino, ndipo ngati angathe amachitapo kanthu.

Koma munthu wosachedwa kutaya mtima amakonda kudziimba mlandu akakumana ndi mavuto. Amaganiza kuti mavuto sangamuthere ndi kuti amachitika chifukwa cha umbuli wake kapena kusaoneka bwino kwake. Motero, amangodziona kuti ndi wolephera.

Kodi munthu wosangalala amakhaladi ndi thanzi ndiponso moyo wabwino? Inde. Chipatala cha Mayo ku Rochester, Minnesota, U.S.A., chinachita kafukufuku kwa zaka 30 pa odwala 800, ndipo anapeza kuti anthu amene sataya mtima amakhala ndi thanzi labwino ndiponso amakhala ndi moyo wautali. Madokotalawa anapezanso kuti anthu amenewa savutika kwambiri ndi nkhawa.

Koma kukhala wosangalala m’dziko limene mavuto akuchulukirachulukirali si chinthu chapafupi. N’chifukwa chake anthu ambiri sachedwa kutaya mtima. Kodi mungatani kuti muthetse vutoli? Bokosi lomwe lili kumanzereli, lili ndi malangizo omwe angakuthandizeni.

Si kuti kukhala wosangalala kungathetseretu mavuto anu onse koma kungakuthandizeni kukhala ndi thanzi ndiponso moyo wabwino. Baibulo limati: “Kukhala wachisoni masiku onse n’koipa, koma wokondwera mtima ali ndi phwando losatha.”—Miyambo 15:15, The Jerusalem Bible.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 26]

Malangizo Othandiza Kukhala ndi Moyo Wosangalala *

▪ Ngati mwayamba kuganiza kuti simungasangalale kapena simungathe kuchita ntchito inayake, thetsani maganizo amenewo mwamsanga. Ndipo ingoganizirani kuti zinthu ziyenda bwino.

▪ Muzisangalala ndi ntchito yanu. Ngakhale ngati ili ndi zina zimene simusangalala nazo, muzingoona mbali zabwinozo.

▪ Muzicheza ndi anzanu amene sataya mtima msanga.

▪ Chitani zinthu zimene mungathe koma zimene simungathe zisiyeni.

▪ Tsiku lililonse lembani zinthu zitatu zimene mwasangalala nazo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Ena a malangizowa atengedwa m’buku lolembedwa ndi madokotala a pa chipatala cha Mayo.