Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?

M’Baibulo muli mfundo zimene zingatithandize kuti Mulungu apitirize kutikonda

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova likulimbikitsa onse amene amakonda Yehova kuti aphunzire zimene angachite kuti aziyendera mfundo za m’Baibulo.

MUTU 1

Chikondi cha Mulungu Sichimatha

Pamafunika khama kuti ubwenzi wathu ndi Mulungu ukhalebe wolimba. Ndiye kodi tingatani kuti zimenezi zitheke?

MUTU 2

Mungatani Kuti Muzikhala Ndi Chikumbumtima Chabwino?

Mulungu anatipatsa chikumbumtima kuti chizititsogolera.

MUTU 3

Anzanu Azikhala Anthu Amene Amakonda Yehova

Anzathu angachititse kuti tizichita zabwino kapena zoipa. Kodi mfundo za m’Baibulo zingatithandize bwanji posankha anzathu?

MUTU 4

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kulemekeza Ulamuliro?

Pali zifukwa zabwino zotichititsa kuti tizilemekeza akuluakulu a boma komanso dongosolo limene Mulungu anakhazikitsa m’banja ndi mumpingo.

MUTU 5

Kodi Tingatani Kuti Tikhale Osiyana Ndi Dzikoli?

Yesu anauza ophunzira ake kuti, “simuli mbali ya dzikoli.” Kodi mawu akuti ‘dziko’ akutanthauza chiyani, nanga n’chifukwa chiyani Akhristu sayenera kukhala mbali ya dziko?

MUTU 6

Kodi Tingasankhe Bwanji Zosangalatsa?

Zosangalatsa zambiri za m’dzikoli zili ngati chipatso chomwe chawola mbali imodzi. Kodi tingatani kuti tizipewa zosangalatsa zoipa?

MUTU 7

Muziona Moyo Ngati Mmene Mulungu Amauonera

Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingatithandize kuti tizisankha bwino pa nkhani zokhudza moyo kapena magazi?

MUTU 8

Yehova Amafuna Kuti Anthu Ake Akhale Oyera

Kuti Yehova azitiona kuti ndife oyera pamafunika zambiri osati kungokhala aukhondo. Kulambira kwathu kuyeneranso kukhala koyera, tiyenera kukhala ndi khalidwe labwino komanso tiyenera kupewa kuganiza zoipa.

MUTU 9

“Thawani Dama”

Kodi dama n’chiyani, nanga tingalipewe bwanji?

MUTU 10

Ukwati Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu

Kodi kukhala pa banja kuli ndi ubwino wotani? Kodi mungasankhe bwanji munthu woyenera kukwatirana naye? Nanga n’chiyani chingathandize kuti banja lisathe?

MUTU 11

Pambuyo pa Tsiku la Ukwati

Banja lililonse limakumana ndi mavuto nthawi zina. Komabe ngakhale banja limene likukumana ndi mavuto aakulu lingathe kukhala lolimba.

MUTU 12

Muzilankhula Mawu “Olimbikitsa”

Zolankhula zathu zingalimbikitse ena koma zingathenso kuwakhumudwitsa. Yehova amatiphunzitsa mmene tingagwiritsire ntchito bwino mphatso yolankhula.

MUTU 13

Kodi Mulungu Amasangalala Ndi Zikondwerero Zonse?

Anthu ambiri amaona kuti zikondwerero ndi maholide ndi zofunika kwambiri. Kodi n’chiyani chingatithandize kudziwa ngati Yehova amasangalala nazo?

MUTU 14

Muzichita Zinthu Zonse Mwachilungamo

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mbali 4 pa moyo wathu, pamene kuchita zinthu mwachilungamo kumakhala kovuta, komanso ubwino wochita zinthu mwachilungamo

MUTU 15

Muzisangalala Ndi Ntchito Yanu

Mlengi wathu amafuna kuti tizisangalala ndi ntchito imene timagwira. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizisangalala ndi ntchito yathu? Kodi pali ntchito imene Akhristu sayenera kugwira?

MUTU 16

Tsutsani Mdyerekezi

Tikukhala m’dziko lomwe anthu ambiri akutsogoleredwa ndi Satana. Kodi tingatani kuti tikhalebe pa ubwenzi ndi Mulungu, nanga tingadziteteze bwanji kwa mdani wa Mulungu ameneyu?

MUTU 17

Mulungu Apitirize Kukukondani

Munthu wina amene analemba nawo Baibulo anauza Akhristu kuti: ‘Dzilimbitseni pamaziko a chikhulupiriro chanu choyera kopambana.’ Kodi mungachite bwanji zimenezi?

Mawu Akumapeto

Tanthauzo la mawu ena opezeka m’buku lakuti Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?