‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’

Bukuli likufotokoza mmene mpingo wa Chikhristu m’nthawi ya atumwi unayambira komanso mmene zochitika za pa nthawi imeneyo zimatikhudzira masiku ano.

Mapu

Mapu osonyeza mayiko otchulidwa m’Baibulo komanso maulendo a Paulo aumishonale.

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzatithandiza pamene tikupitiriza ‘kuchitira umboni mokwanira za Ufumu wa Mulungu’?

MUTU 1

“Pitani Mukaphunzitse Anthu . . . Kuti Akhale Ophunzira Anga”

Yesu ananeneratu kuti uthenga wa Ufumu udzalalikidwa kwa anthu a mitundu yonse. Kodi mawuwa akukwaniritsidwa bwanji?

MUTU 2

“Mudzakhala Mboni Zanga”

Mmene Yesu anathandizira atumwi ake kuti adzatsogolere pa ntchito yolalikira.

MUTU 3

“Anadzazidwa ndi Mzimu Woyera”

Kodi mzimu woyera wa Mulungu unathandiza bwanji pamene mpingo wa Chikhristu unkakhazikitsidwa?

MUTU 4

“Osaphunzira Ndiponso Anthu Wamba”

Atumwi anachita zinthu molimba mtima ndipo Yehova anawadalitsa.

MUTU 5

“Ife Tiyenera Kumvera Mulungu Monga Wolamulira”

Atumwi anachita zinthu molimba mtima ndipo anapereka chitsanzo kwa Akhristu onse oona.

MUTU 6

“Sitefano Anali ndi Mphamvu Ndipo Ankachita Kuonekeratu Kuti Mulungu Ali Naye”

Kodi zimene Sitefano anachita pochitira umboni molimba mtima zingatiphunzitse chiyani?

MUTU 7

Kulalikira “Uthenga Wabwino Wonena za Yesu”

Filipo anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yolalikira.

MUTU 8

Mpingo “Unayamba Kukhala Pamtendere”

Saulo, amene ankazunza kwambiri Akhristu, anakhala mtumiki wa Mulungu wakhama kwambiri.

MUTU 9

“Mulungu Alibe Tsankho”

Akhristu anayamba kulalikira kwa anthu osadulidwa a mitundu ina.

MUTU 10

“Mawu a Yehova Anapitiriza Kufalikira”

Petulo anapulumutsidwa, ndipo kuzunzidwa kwa ophunzira a Khristu sikunalepheretse kufalikira kwa uthenga wabwino.

MUTU 11

“Anapitiriza Kukhala Osangalala Komanso Mzimu Woyera Unkawathandiza Kwambiri”

Zimene tingaphunzire kwa Paulo ngati anthu sakufuna kumvetsera uthenga wabwino.

MUTU 12

“Ankalankhula Molimba Mtima Chifukwa cha Mphamvu ya Yehova”

Paulo ndi Baranaba anasonyeza kuti anali odzichepetsa, opirira komanso olimba mtima.

MUTU 13

“Sanagwirizane Nazo”

Nkhani ya mdulidwe inapita ku bungwe lolamulira.

MUTU 14

“Tonse Tagwirizana”

Onani zimene bungwe lolamulira linachita kuti ligwirizane chimodzi pa nkhani ya mdulidwe, ndipo zimenezi zinathandiza kuti m’mipingo mukhale mgwirizano.

MUTU 15

“Ankalimbikitsa Mipingo”

Atumiki oyendayenda anathandiza mipingo kuti ikhalebe yolimba m’chikhulupiriro.

MUTU 16

“Wolokerani ku Makedoniya Kuno”

Anthu ambiri anadalitsidwa chifukwa Paulo limodzi ndi anzake anavomera kuchita utumiki womwe anapatsidwa ndipo anakhalabe osangalala ngakhale pamene ankazunzidwa.

MUTU 17

“Anakambirana Nawo Mfundo za M’Malemba”

Paulo anachitira umboni mokwanira kwa Ayuda a ku Tesalonika ndi ku Bereya.

MUTU 18

‘Funafunani Mulungu ndi Kumupezadi’

Kodi kutchula mfundo zimene omvera ake ankagwirizana nazo, kunathandiza bwanji Paulo kuyamba kulalikira?

MUTU 19

‘Pitiriza Kulankhula, Usakhale Chete’

Kodi tikuphunzira chiyani kuchokera pa zimene Paulo ankachita ku Korinto, zomwe zingatithandize kuti tidzichitira umboni mokwanira za Ufumu wa Mulungu?

MUTU 20

“Anapitiriza kufalikira Ndipo Sankagonjetseka” Ngakhale Kuti Panali Otsutsa

Onani mmene Apolo ndi Paulo anathandizira kuti uthenga wabwino ufalikire.

MUTU 21

“Ndilibe Mlandu wa Magazi a Anthu Onse”

Paulo anapereka malangizo kwa akulu mumpingo komanso anali wakhama pochita utumiki wake.

MUTU 22

“Chifuniro cha Yehova Chichitike”

Paulo anali wofunitsitsa kuchita chifuniro cha Mulungu ndipo anapita ku Yerusalemu.

MUTU 23

“Mvetserani Mawu Anga Odziteteza”

Paulo anateteza choonadi pamaso pa magulu a anthu achiwawa ndiponso Khoti Lalikulu la Ayuda.

MUTU 24

“Limba Mtima”

Paulo anapulumuka chiwembu chofuna kumupha komanso analankhula mawu odziteteza pamaso pa Bwanamkubwa Felike.

MUTU 25

“Ndikuchita Apilo Kuti Ndikaonekere kwa Kaisara”

Paulo anatipatsa chitsanzo cha mmene tingatetezere uthenga wabwino.

MUTU 26

“Palibe Amene Ataye Moyo Wake”

Ngalawa imene Paulo anakwera itasweka, iye anasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro cholimba komanso ankakonda anthu.

MUTU 27

“Anachitira Umboni Mokwanira”

Paulo anapitiriza kulalikira pamene anali m’ndende ku Roma.

MUTU 28

“Mpaka Kumalekezero a Dziko Lapansi.”

A Mboni za Yehova akupitiriza kugwira ntchito imene otsatira a Yesu Khristu ankagwira m’nthawi ya atumwi.

Mlozera wa Zithunzi

Zithunzi zofunika kwambiri zomwe zagwiritsidwa ntchito m’bukuli.