Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Abale sanasiye kutumikira Yehova ngakhale kuti anthu ena ankawononga katundu wawo

GEORGIA | 1998-2006

Sanasiye Kutumikira Yehova Ngakhale Kuti Ankaopsezedwa

Sanasiye Kutumikira Yehova Ngakhale Kuti Ankaopsezedwa

Abale ndi alongo a m’dziko la Georgia sanachite mantha ndipo anapitirizabe kuchita misonkhano. Akulu ankayesetsa kuchita zinthu mosamala kuti asaike ofalitsa pa mavuto. M’bale André Carbonneau wa ku Canada, yemwe ndi loya, ankateteza abale ndi alongo pa milandu yosiyanasiyana. M’baleyu anati: “Abale ankachita zinthu mochenjera kwambiri akamachita misonkhano, ndipo ankasankha m’bale mmodzi kuti aime kumsewu. M’baleyo ankakhala ndi foni ndipo akaona kuti gulu la anthu olusa likubwera, ankadziwitsa akulu.”

Anthu ena olusa anawotcha nyumba ya banja la a Shamoyan (kumanzere) komanso malo ofikira mabuku (kumanja)

Gulu la anthu olusa likamenya kapena kuwopseza abale, ofesi ya nthambi inkatumiza abale awiri kuti akawalimbikitse. M’bale André anati: “Zinkakhala zolimbikitsa kwambiri. Abale ochokera ku ofesi akafika, ankapeza kuti abale ndi alongo ambirimbiri asonkhana ndipo ankadabwa kwambiri chifukwa anthuwo ankaonekabe osangalala.”

Abale ankazunzidwa kwambiri ngakhale m’khoti

Nawonso anthu amene sanamenyedwe kapena kuwopsezedwa mwachindunji, kuphatikizapo ophunzira Baibulo, ankaonekabe osangalala. Pa nthawi ina M’bale André anacheza ndi mayi wina yemwe anali atatsala pang’ono kukhala wofalitsa wosabatizidwa. Mayiyo anauza m’baleyu kuti: “Ndikamaona pa TV a Mboni akumenyedwa ndi magulu olusa a zipembedzo zina, ndinkaona kuti chipembedzo cha Mboni za Yehova ndi choona, moti nanenso ndikufuna nditakhala wa Mboni.”

Maloya Ankateteza Abale Awo Molimba Mtima

Pa zaka zovutazi, abale anali ndi chikhulupiriro cholimba kwambiri ndipo sanasiye kulalikira. Komanso abale ndi alongo omwe anali maloya, anasonyeza kulimba mtima ndiponso chikhulupiriro.

Anthu ankanena zinthu zambiri zabodza zokhudza a Mboni za Yehova pa TV komanso wailesi. Ankanena kuti a Mboni za Yehova amathetsa mabanja, ndi oukira boma ndiponso amakana kulandira thandizo lakuchipatala. Maloya amene ankateteza abale athu kukhoti pa milandu ya nkhani ngati zimenezi, ankakumana ndi mavuto ambiri. Mwachitsanzo, mbiri yawo inkatha kuipa komanso ntchito yawo inkakhala pangozi.

Abale a m’Dipatimenti ya Zamalamulo ochokera ku ofesi ya nthambi ya ku United States ankateteza abale ndi alongo awo kukhoti

M’bale John Burns, yemwe anali loya wochokera ku ofesi ya nthambi ya ku Canada, anathandizanso kwambiri abale ndi alongo pa nthawiyi. M’bale Burns anati: “Abale ndi alongo a m’dzikoli omwe anali maloya anadzipereka kuthandiza abale awo. Ngakhale kuti ankadziwa zoti mbiri yawo ikhoza kuipa, sankachita mantha kuimira abale awo kukhoti ndipo ankalimba mtima kunena kuti nawonso ndi a Mboni za Yehova.” Abale ndi alongo amenewa anathandiza kwambiri “kukhazikitsa mwalamulo ntchito ya uthenga wabwino.”Afil. 1:7.

Anthu Ambiri a ku Georgia Sankagwirizana ndi Nkhanza Zomwe Magulu Ena Ankachitira a Mboni

Nkhanzazi zinapitirirabe, choncho kungoyambira pa 8 January, 2001, a Mboni za Yehova anayamba kuyenda ndi chikalata ndipo ankapempha anthu osiyanasiyana kuti anene maganizo awo pa nkhanza zomwe anthu ankawachitira. Ankafuna kuti anthuwa akasayina chikalatachi akachipereke kuboma.

M’bale Burns anati: “Cholinga chathu popempha anthu kuti asayine chikalatachi chinali kufuna kuthandiza anthu kudziwa kuti anthu ambiri a ku Georgia sankagwirizana ndi nkhanzazi. Tinkafunanso kuthandiza anthu kudziwa kuti amene ankachita nkhanzazi anali anthu a m’kagulu kena kachipembedzo.”

Pamene milungu iwiri inkatha, anthu okwana 133,375 a m’madera onse a dziko la Georgia anali atasainira chikalatachi. Ambiri mwa anthuwa anali a tchalitchi cha Orthodox. Kenako anachipereka kwa Pulezidenti Shevardnadze, komabe zinthu zamtopola zimene anthuwa ankachita sizinathe. Anthu a m’kagulu kachipembedzo kaja anapitirizabe kuchitira nkhanza a Mboni za Yehova, ndipo nthawi zambiri ankachita zimenezi mwadala kuti aone zimene zingachitike.

Anthu ambirimbiri a ku Georgia anasaina zikalata zosonyeza kuti sakugwirizana ndi nkhanza zimene anthu ankachitira a Mboni za Yehova

Koma Yehova sanasiye atumiki ake ndipo anapitirizabe kuwadalitsa. Pa nthawi imene gulu la chipembedzo lija linkavutitsa atumiki a Mulungu, Yehova sanasiye kukoka anthu a mitima yabwino kuti alowe m’gulu lake.

Anasiya Chipembedzo Chabodza

Kwa zaka zambiri, Mayi Babilina Kharatishvili anali wodzipereka kwambiri kutchalitchi chawo cha Orthodox. Ali ndi zaka za m’ma 30, mayiwa ankayenda m’midzi n’kumaphunzitsa anthu zokhudza anthu oyera mtima.

Komabe, Mayi Babilina ankafunitsitsa atadziwa zambiri zokhudza Mulungu. Choncho tsiku lina anaganiza zopita kuseminale ina ya tchalitchi ya Orthodox. Kumeneko m’busa wina anatulutsa buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha ndipo analimbikitsa anthu onse kuti apeze bukuli kuchokera kwa a Mboni za Yehova. M’busayo anati: “Buku limeneli lingakuphunzitseni zambiri zokhudza Baibulo.”

Mayi Kharatishivili atamva zimenezi anadzidzimuka kwambiri. M’mbuyomu mayiwa ankakana kucheza ndi a Mboni za Yehova, koma apa tsopano anamva kuchokera kwa m’busa wa tchalitchi chawo kuti mabuku a Mboni ndi abwino kwambiri. Ndiyeno mayiwa anadzifunsa kuti: ‘Ngati mabuku a Mboni ndi amene angandithandize kudziwa Mulungu, ndiye ndikuchita chiyani kuno?’ Atangochoka kumeneko anayamba kufufuza a Mboni za Yehova m’tauni ya Poti ndipo atawapeza, anayamba kuphunzira Baibulo.

Mayiwa anaphunzira zambiri ndipo anayamba kusintha moyo wawo. Pa nthawi ina anati: “Nditaphunzira m’Baibulo kuti Mulungu amadana ndi kulambira mafano, ndinasiya nthawi yomweyo kulambira mafano. Ndinkaona kuti ndiyenera kuchita zimenezi basi.” Pamene Mayi Babilina ankaganiza zoti akhale a Mboni za Yehova n’kuti ali ndi zaka za m’ma 70.

Mayi Babilina Kharatishivili ankauza mdzukulu wawo, dzina lake Izabela, zimene ankaphunzira m’Baibulo

N’zomvetsa chisoni kuti Mayi Babilina anadwala kwambiri ndipo anamwalira m’chaka cha 2001 asanabatizidwe. Patapita nthawi mdzukulu wawo wa mayiwa, dzina lake Izabela, anabatizidwa ndipo mpaka pano akutumikirabe Yehova mokhulupirika.

Ankafuna Kukhala Sisitere

Mayi Eliso Dzidzishvili ali ndi zaka 28 anaganiza zokhala sisitere. Mu 2001 anasamukira ku Tbilisi chifukwa m’tauni yakwawo ya Tkibuli kunalibe nyumba ya masisitere. Pamene ankadikirira kuti kalata yawo yofunsira usisitere iyankhidwe, anayamba ntchito yophunzitsa pasukulu ina yomwe sinali ya boma. M’kalasi imene ankaphunzitsa munali mwana wa Mboni dzina lake Nunu.

Mayi Dzidzishvili anati: “Ndinkacheza ndi Nunu nkhani za m’Baibulo. Pa nthawiyo ndinkakwiya kwambiri munthu wina akamandiuza zinthu zina zosemphana ndi zimene tinkakhulupirira m’chipembedzo chathu cha Orthodox. Komabe Nunu ankandionetsa zimene Baibulo limanena ndipo ankachita zimenezi moleza mtima kwambiri. Tsiku lina anandipempha kuti ndiwerenge naye limodzi kabuku kakuti, Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Titawerenga kabukuka komanso mavesi a m’Baibulo, ndinazindikira kuti kulambira mafano n’kusamvera lamulo la Mulungu.”

Kenako, Mayi Dzidzishvili anapita kutchalitchi kwawo n’kukafunsa abusa mafunso ena ndi ena okhudza zimene amakhulupirira. Zimene m’busayo ananena zinawatsimikizira kuti zomwe ankakhulupirira kutchalitchi kwawoko si zogwirizana ndi zimene Baibulo limanena. (Maliko 7:7, 8) Apa anazindikira kuti apeza chipembedzo cholondola, moti nthawi yomweyo anayamba kuphunzira Baibulo. Patapita nthawi anabatizidwa n’kukhala a Mboni za Yehova.

A Eliso Dzidzishvili (kumanzere), omwe ankafuna kukhala sisitere. Nunu Kopaliani (kumanja)

Anamanga Nyumba za Ufumu Ngakhale Kuti Ankatsutsidwa

Pamene chaka cha 2001 chinkafika, mipingo yambiri inalibe malo abwino ochitiramo misonkhano. Kafukufuku anasonyeza kuti pankafunika Nyumba za Ufumu zokwana 70. Choncho, ntchito yomanga Nyumba za Ufumu inayambika ngakhale kuti ankatsutsidwa.Ezara 3:3.

Pasanapite nthawi yaitali, kagulu kena komanga Nyumba za Ufumu kanayamba kukonzanso nyumba ina yomwe mipingo ingapo inkagwiritsa ntchito mumzinda wa Tbilisi. Kenako anamanga Nyumba za Ufumu ziwiri, ina ku Tbilisi ndipo ina m’tauni ya Chiatura, yomwe ili m’chigawo chakumadzulo kwa dziko la Georgia.

Nyumba ya Ufumu ya ku Tbilisi (kumanzere) inagumulidwa ndipo panamangidwa ina (kumanja)

M’bale Tamazi Khutsishvili, yemwe anamanga nawo Nyumba ya Ufumu ku Chiatura, anati: “Pa gulu lathu tinalipo anthu 15 ndipo tinkapita kukamanga Nyumba ya Ufumuyo tsiku lililonse. Sipanatenge nthawi kuti anthu a m’deralo azindikire kuti tikumanga Nyumba ya Ufumu. Nthawi zina tikamagwira ntchito, tinkamva zoti kubwera gulu la anthu kudzagumula nyumba imene tinkamangayo.”

Ndiye kodi zinthu zinayenda bwanji? M’bale Khutsishvili ananena kuti: “Tinapitirizabe kumanga ndipo pamene miyezi itatu inkatha, tinali titamaliza. Tinazindikira kuti ankangofuna kuti tibooke m’mimba, chifukwa palibe amene anabwera kudzagumula nyumbayo.” *

Abale Anapeza Mpumulo

Anthu a m’gulu la chipembedzo cha Orthodox atamangidwa pamodzi ndi mtsogoleri wawo, Vasili Mkalavishvili

Mu October 2003, abale anayamba kumanga Nyumba ya Ufumu mumzinda wa Samtredia. Ntchitoyi ili mkati, anthu ena anayamba kuwawopseza kuti agwetsa nyumbayo. Ndiyeno makoma a nyumbayo atakwera ndithu, anthu ena anabwera n’kudzagumula.

Koma mu November 2003, m’dziko la Georgia munachitika zinthu zina zomwe zinachititsa kuti mitima ya abale ikhale pansi. Boma litasintha, zinthu zinasinthanso moti anthu anayamba kukhala ndi ufulu wolambira. Kusintha kumeneku kunachititsa kuti anthu angapo a m’gulu la chipembedzo cha Orthodox amangidwe. Anthuwa anamangidwa chifukwa ankazunza a Mboni za Yehova.

Anthu a Mulungu Anadalitsidwa Kwambiri

Anthu atangosiya kuchitira nkhanza a Mboni za Yehova ku Georgia, abale ndi alongo anadalitsidwa kwambiri. Mwachitsanzo, pamsonkhano wachigawo wa mu 2004, panatulutsidwa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu lachijojiya.

Chinthu china chosaiwalika chinachitika pamsonkhano wachigawo wa mu 2006, womwe unali ndi mutu wakuti, “Chipulumutso Chayandikira.” Pamsonkhanowu M’bale Geoffrey Jackson, yemwe ali m’Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani yosaiwalika. Akukamba nkhaniyo, M’bale Jackson analengeza za kutulutsidwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lachijojiya. Anthu omwe anali pamsonkhanowo anasangalala kwambiri ndi chilengezo chimenechi.

Kutulutsidwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano lachijojiya mu 2006

Anthu ena analephera kudzigwira moti anayamba kugwetsa misozi chifukwa cha chisangalalo. Mlongo wina anati: “Sindingakwanitse kufotokoza chisangalalo chimene ndinali nacho pamene ndinalandira Baibulo langa. . . . Msonkhano umenewu ndi wosaiwalika.” Pamsonkhanowu panali anthu oposa 17,000, ndipo msonkhano ngati umenewu unali usanachitikeponso ku Georgia.

^ ndime 29 Kungochokera mu 2001 kufika mu 2003, m’dziko la Georgia munamangidwa Nyumba za Ufumu zokwana 7.