Onani zimene zilipo

Kodi Mulungu Anaseŵenzetsa Cisanduliko Polenga Zamoyo Zosiyanasiyana?

Kodi Mulungu Anaseŵenzetsa Cisanduliko Polenga Zamoyo Zosiyanasiyana?

Yankho la m’Baibo

 Iyai. Baibo imaonetsa bwino kuti Mulungu anacita kulenga anthu, kuphatikizapo zinyama na zomela zosiyanasiyana. * (Genesis 1:12, 21, 25, 27; Chivumbulutso 4:11) Imakambanso kuti mtundu wonse wa anthu unacokela kwa makolo athu oyambilila, Adamu na Hava. (Genesis 3:20; 4:1) Baibo siicilikiza maganizo akuti Mulungu anaseŵenzetsa cisanduliko polenga zamoyo zamitundu yosiyanasiyana. Koma Baibo siimatsutsa zimene asayansi amakamba zakuti zamoyo. *

 Kodi Mulungu anaseŵenzetsa cisanduliko?

 Anthu amene amakhulupilila kuti Mulungu anaseŵenzetsa cisanduliko kuti alenge zamoyo, amakhalanso na maganizo osiyana mmene anacitila zimenezo. Malinga na buku lakuti Encyclopædia Britannica, “anthu amakhulupilila kuti Mulungu amatsogolela cilengedwe conse malinga na mmene zinthu ziyendela m’cilengedwe.”

 Zimene anthu amakhulupilila zimaphatikizapo izi:

  •   Zamoyo zonse zinacokela ku zinthu zakale-kale kwambili.

  •   Camoyo cingasinthiletu n’kukhala camoyo cina (macroevolution).

  •   Mulungu mwina ndiye amene amasandulitsa zinthu m’cilengedwe.

 Kodi cisanduliko n’cogwilizana na Baibo?

 Kukhulupilila cisanduliko kungaonetse kuti zimene Baibo imakamba za kulenga m’buku la Genesis n’zosalondola. Komabe, Yesu anaonetsa kuti mfundo zimene zili mu Genesis n’zazoona. (Genesis 1:26, 27; 2:18-24; Mateyu 19:4-6) Baibo imakamba kuti Yesu anali kukhala kumwamba na Mulungu asanabwele padziko lapansi, ndipo anathandiza Mulungu kuti zonse ‘zikhalepo.’ (Yohane 1:3) Conco maganizo akuti Mulungu anaseŵenzetsa cisanduliko polenga zamoyo zosiyanasiyana, n’yosagwilizana na zimene Baibo imaphunzitsa.

 Zomela komanso zinyama zimasintha kuti zipitilize kukhala na moyo malo akasintha, kodi ndiye kuti ici n’citsanzo ca kusandulika?

 Baibo siimafotokoza kwambili kusiyana kumene kungakhalepo pa colengedwa ca mtundu winawake. Komanso siimatsutsa mfundo yakuti zinyama zosiyanasiyana na zomela zimene Mulungu analenga zingasinthe pofuna kuzoloŵela malo atsopano kumene zili. Ngakhale kuti ena amaona kusintha kumeneko monga kusandulika, pamakhala palibe colengedwa catsopano camtundu winawake.

zilizonse n’zosiyana na zinzake ngakhale za mtundu umodzi.

^ ndime 1 Baibo limaseŵenzetsa liwu lakuti “mtundu” limene limatanthauza zambili kuposa liwu lacingelezi lakuti “species” limene asayansi amasewenzetsa. Kambili zimene asayansi amati ni kusandulika kukhala mtundu watsopano zimangokhala kusiyanako cabe kwa zamoyo za mtundu umodzi, monga mmene liwuli analisewenzetsela mu buku la Genesis.

^ ndime 1 Izi n’zimene anthu amati kusandulika pa mlingo wocepa (microevolution).