Onani zimene zilipo

Kodi Baibo Ingathandize Anthu Odwala Matenda Osathelapo?

Kodi Baibo Ingathandize Anthu Odwala Matenda Osathelapo?

Yankho la m’Baibo

 Inde. Mulungu amasamalila atumiki ake amene akudwala. Ponena za mtumiki wokhulupilika wina, Baibo imati: “Yehova adzacilikiza wonyozekayo pamene akudwala pabedi lake.” (Salimo 41:3) Conco, ngati muli na matenda osathelapo, njila zitatu zotsatilazi zingakuthandizeni:

  1.   Pemphelelani mphamvu kuti mupilile. “Mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse,” ungakuthandizeni kucepetsa nkhawa. Ndipo mungakondwele na umoyo ngakhale muli na mavuto.—Afilipi 4:6, 7.

  2.   Muzikhalako na maganizo wosangalala. Baibo imati: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ocilitsa, koma mtima wosweka umaumitsa mafupa.” (Miyambo 17:22) Kukhalako wosangalala kungakuthandizeni kucepetsa cisoni, komanso zingakhale zopindulitsa ku thanzi lanu.

  3.   Khalani na cikhulupililo m’malonjezo a Mulungu a kutsogolo. Kukhala na ciyembekezo cabwino ca zamtsogolo, kungakuthandizeni kukhala wokondwela olo kuti muli na matenda osathelapo. (Aroma 12:12) Baibo inakambilatu za nthawi pamene “Palibe munthu adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’” (Yesaya 33:24) Mulungu adzacotsapo matenda onse amene anthu alephela kuthetsa. Mwacitsanzo, Baibo imakamba kuti okalamba adzabwelela kuunyamata. Imati: “Mnofu wake usalale kuposa mmene unalili ali mnyamata. Abwelele ku masiku ake aunyamata pamene anali ndi mphamvu.”—Yobu 33:25.

 Dziŵani izi: Ngakhale kuti Mboni za Yehova zimadalila thandizo la Yehova, zimafunanso cithandizo ca cipatala pa matenda osathelapo. (Maliko 2:17) Komabe, sitikakamiza anthu kulandila cithandizo cinacake ca cipatala, cifukwa munthu aliyense ayenela kupanga yekha cosankha pa nkhani zimenezi.