Onani zimene zilipo

Nyumba zili m’madzi osefukila mu mzinda wa Rivers State, ku Nigeria

NOVEMBER 13, 2020
NIGERIA

Kusefukila Koopsa kwa Madzi ku Nigeria

Kusefukila Koopsa kwa Madzi ku Nigeria

Kugwa kwa cimvula cacikulu m’miyezi ya September na October 2020, kwacititsa kuti madzi asefukile kwambili m’mizinda ingapo m’dziko la Nigeria. Madzi osefukilawa asakaza mafamu na nyumba zambili. N’zacisoni kuti mmodzi wa abale athu, anamwalila cifukwa ca tsoka limeneli. Kuwonjezela apo, ofalitsa opitilila 1,828 anasiya nyumba zawo. Ndipo nyumba zoposa 62 za abale athu zinawonongeka.

Nyumba ya Ufumu ili m’madzi osefukila mu mzinda wa Delta State, ku Nigeria

Ofesi ya Nthambi ya ku Nigeria inakhazikitsa Makomiti 7 Othandizila Pakagwa Tsoka kuti atsogolele nchito yopeleka cithandizoyi, mogwilizana na ndondomeko za citetezo za COVID-19. Oyang’anila madela na akulu kumeneko, akupeleka thandizo lakuthupi komanso lakuuzimu kwa abale na alongo amene akhudzidwa na tsokali.

Tili acisoni kuti anthu ena ataya miyoyo yawo cifukwa ca tsokali. Koma tidziŵa kuti Yehova, Mulungu wathu wotipulumutsa, adzapitiliza kutonthoza na kuthandiza abale athu pa nthawi ino yovuta.—Salimo 68:19.