Imbilani Yehova—Nyimbo Zatsopano

Sangalalani ndi nyimbo zatsopanozi potamanda ndi kulambila Yehova Mulungu. Citani daunilodi nyimbo zamalimba na mau ake, ndi kumaziimba mosangalala.

SONG 136

Ufumu Ulamulila​—Ubwele!

Nyimbo yaulemelelo yotamanda Yehova Mulungu ndi kulengeza Ufumu wa Khristu Yesu.

NYIMBO 137

Tilimbitseni Mtima

Imbani nawo pamodzi nyimbo yopempha Yehova kuti atilimbitse mtima polalikila za iye.

SONG 138

Dzina lanu ndimwe Yehova

Tamandani dzina la Yehova lolemekezeka, ndipo anthu adziŵe kuti ni Wam’mwambamwamba.

NYIMBO 139

Aphunzitseni Kucilimika

Pempho kwa Yehova Mulungu kuti atiteteze na kutithandiza kupilila mokhulupilika pa mpikisano wa moyo.

NYIMBO 140

Umoyo wa Mpainiya

Imbani za cikondi canu kwa Yehova ndi cisangalalo canu pa nchito yokondweletsa na umoyo umene mukonda.

NYIMBO 141

Kusakila anthu okonda mtendele

Nyimbo yotsitsimula ndi yokondweletsa yonena za mmene timakondela anthu, na khama lathu posakila nkhosa za Mulungu za mtengo wapatali.

NYIMBO 142

Tilalikile kwa Anthu a Makhalidwe Onse

Imbani za ubwino wa Yehova na mmene timalandilila anthu a makhalidwe onse kuti akhale mabwenzi a Mulungu.

NYIMBO 143

Kuwala m’Dziko la Mdima

Uthenga wathu umati ngwee mu mdima.

NYIMBO 144

Ni Moyo Wawo

Tilalikile uthenga wa Mulungu kukali nthawi.

NYIMBO 145

Kukonzeka Kukalalikila

Sitilabadila kuwama kwa m’nyumba, timalimbabe mtima kuti mpaka tikalalikile.

NYIMBO 146

Munacitila Ine

Kwa Yesu, nchito ya cikondi iliyonse ndi thandizo limene tinapeleka kwa abale ake okondedwa, tinacitila iye.

NYIMBO 147

Cuma Capadela

Yehova amakonda ana ake odzozedwa na mzimu, nawonso amakonda kucita cifunilo cake.

NYIMBO 148

Munapeleka Mwana Wanu Wobadwa Yekha

Yamikani Yehova cifukwa ca mphatso yamtengo wapatali imene anatipatsa. Mphatsoyi imapeleka ciyembekezo kwa onse ndi kutitsegulila mwayi wodzakhala na Moyo.

NYIMBO 149

Tikuyamikani Cifukwa ca Dipo

Dipo ni cikondi copambana koposa, ndipo tidzayamikila Yehova kwamuyaya.

NYIMBO 150

Kudzipeleka na Mtima Wonse

Dzipelekeni potumikila Yehova mokondwa m’njila iliyonse imene afuna kukuseŵenzetsani.

NYIMBO 151

Ana a Mulungu Adzaonekela

Tiyembekezela mwacidwi tsiku limene Yehova adzakwezela kumwamba abale a Yesu kaamba ka cipambano ndi mphoto yawo.

NYIMBO 152

Ndimwe Mphamvu Zathu, Ciyembekezo, na Cidalilo Cathu

Tikakhala na nkhawa, Mulungu angakhale mphamvu zathu, ciyembekezo, na cidalilo cathu

NYIMBO 153

Kodi Mumamvela Bwanji?

Kodi mumamvela bwanji mukadziŵa kuti anthu oona mtima mwawafika pamtima?

NYIMBO 154

Tidzapilila Mosalekeza

Nyimbo yotithandiza kupilila zovuta na kutumikila Yehova mokhulupilika nthawi zonse.