Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 96

Buku lake la Mulungu ni Cuma

Buku lake la Mulungu ni Cuma

(Miyambo 2:1)

  1. 1. Pali buku limene mau ake,

    Tikaŵelenga timakondwela.

    Mfundo zake zodabwitsa n’zamphamvu;

    Zimatipatsa ciyembekezo.

    Bukulo ndilo Baibo yoyela

    Analemba anauzilidwa.

    Anali amuna okonda M’lungu.

    Analemba mwa mphamvu ya mzimu.

  2. 2. Analemba nkhani za cilengedwe,

    Mmene M’lungu anacipangila.

    Analemba za moyo m’paradaiso

    Komanso mmene unasinthila.

    Analemba za mngelo wina wake

    Amene anatsutsa Yehova.

    Izi zinabweletsadi mavuto

    Koma Yehova adzapambana.

  3. 3. Lomba yafika nthawi tikondwele,

    Yesu wayamba kulamulila.

    Tilalikile uthenga wabwino

    Wonena za Ufumu wa M’lungu.

    M’buku lake muli zosangalatsa;

    Mulidi cakudya coculuka.

    Limatipatsa mtendele wambili.

    Tifunika tiziliŵelenga.

(Onaninso 2 Tim. 3:16; 2 Pet. 1:21.)