Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 57

Tilalikile kwa Anthu a Makhalidwe Onse

Tilalikile kwa Anthu a Makhalidwe Onse

(1 Timoteyo 2:4)

  1. 1. Tikhale anthu osakondela.

    Tikhale monga Mulungu wathu.

    Afuna onse apulumuke

    Na kukhala atumiki ake.

    (KOLASI)

    Si malo koma munthu;

    Si nkhope koma mtima.

    Tiuze anthu onse co’nadi.

    Timasakila anthu,

    Amene amafuna:

    “Kukhala mabwenzi a Yehova.”

  2. 2. Si kanthu mmene aonekela.

    Si kanthu kumene acokela.

    Mtima wawo ndiwo wofunika—

    Ni umene Yehova aona.

    (KOLASI)

    Si malo koma munthu;

    Si nkhope koma mtima.

    Tiuze anthu onse co’nadi.

    Timasakila anthu,

    Amene amafuna:

    “Kukhala mabwenzi a Yehova.”

  3. 3. Yehova amalandila onse

    Ofuna kukhala anthu ake.

    Tilalikile kwa anthu onse,

    Tiŵauze uthenga wabwino.

    (KOLASI)

    Si malo koma munthu;

    Si nkhope koma mtima.

    Tiuze anthu onse co’nadi.

    Timasakila anthu,

    Amene amafuna:

    “Kukhala mabwenzi a Yehova.”

(Onaninso Yoh. 12:32; Mac. 10:34; 1 Tim. 4:10; Tito 2:11.)