Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 19

Mgonelo wa Ambuye

Mgonelo wa Ambuye

(Mateyu 26:26-30)

  1. 1. Atate ise tasonkhana

    Pa tsiku lopatulika.

    Imwe munasankha kuti muonetse

    Cikondi canu kwa anthu.

    Mwana wa nkhosa anadyewa,

    Kumasula anthu anu.

    Yesu modzipeleka anatifela,

    Kukwanilitsa ulosiwo.

  2. 2. Yesu anapeleka moyo

    Kuti atipulumutse.

    Tikaona vinyo na mkate tidziŵa,

    Ukulu wa mphatso iyi.

    Timakumbukila tsikuli

    Na mtima woyamikila.

    Cifukwa tidziŵa kuti mphatso iyi

    Inatimasula ku imfa.

  3. 3. Tasonkhana pamaso panu,

    Kuti’se tiyamikile,

    Cikondi cimene munationetsa

    Potumiza mwana wanu.

    Tidziŵa kuti tsiku iyi

    Imakulemekezani.

    Tikapitiliza kutsatila Yesu,

    Tidzapeza moyo wosatha.

(Onaninso Luka 22:14-20; 1 Akor. 11:23-26.)