Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 131

“Cimene Mulungu Wacimanga Pamodzi”

“Cimene Mulungu Wacimanga Pamodzi”

(Mateyu 19:5, 6)

  1. 1. Anthu na Mulungu,

    Acita umboni,

    Za cikwati ca lelo,

    Comangidwa bwino.

    (KOLASI 1)

    Mwamuna walonjeza

    Kukonda mkaziyu.

    “Ngati M’lungu wamanga,

    Musalekanitse.”

  2. 2. Onse aphunzila,

    Mau a Yehova.

    Lomba ayembekeza,

    Dalitso la M’lungu.

    (KOLASI 2)

    Mkazinso walonjeza

    Kukonda mwamuna.

    “Ngati M’lungu wamanga,

    Musalekanitse.”

(Onaninso Gen. 2:24; Mlal. 4:12; Aef. 5:22-33.)