Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 120

Tengelani Kufatsa kwa Khristu

Tengelani Kufatsa kwa Khristu

(Mateyu 11:28-30)

  1. 1. Yesu anali wopambana m’zonse.

    Koma sananyade, sanadzikweze.

    Modzicepetsa anadzipeleka,

    Kucita cifunilo ca Yehova.

  2. 2. Olemedwa na nkhawa zosautsa,

    Adzaŵathandiza kuthetsa nkhawa.

    Ndipo iwo adzatsitsimulidwa

    Akafuna za Ufumu coyamba.

  3. 3. Yesu anati ‘se ndise abale.

    Tisadzikweze tikhale ofatsa.

    Yehova M’lungu adzatidalitsa,

    Tidzapezadi moyo wamuyaya.

(Onaninso Miy. 3:34; Mat. 5:5; 23:8; Aro. 12:16.)