Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 118

“Tiwonjezeleni Cikhulupililo”

“Tiwonjezeleni Cikhulupililo”

(Luka 17:5)

  1. 1. O Yehova, ise ndise ocimwa,

    Mtima wathu ‘mafuna zoipa.

    Nthawi zina ise zimativuta

    Kukhala na cikhulupililo.

    (KOLASI)

    O Yehova, ise tikupemphani

    Kuti mumvele pemphelo lathu.

    M’tiwonjezele cikhulupililo,

    Kuti’se tikulemekezeni.

  2. 2. Ngati tilibe cikhulupililo

    N’covuta kukukondweletsani.

    Koma ngati timakhulupilila,

    Tidzatumikila mosaopa.

    (KOLASI)

    O Yehova, ise tikupemphani

    Kuti mumvele pemphelo lathu.

    M’tiwonjezele cikhulupililo,

    Kuti’se tikulemekezeni.

(Onaninso Gen. 8:21; Aheb. 11:6; 12:1.)