Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Pindulani na Nsembe ya Yesu

Pindulani na Nsembe ya Yesu

 Kamodzi pa caka, Mboni za Yehova komanso anthu mamiliyoni amene amaitanidwa, amasonkhana padziko lonse kuti acite Cikumbutso ca imfa ya Yesu monga mmene iye analamulila. (Luka 22:19) Cocitika cimeneci cimatithandiza kuyamikila zimene Yesu anaticitila popeleka moyo wake kaamba ka anthu. Cimationetsanso mmene nsembe yake ingatithandizile pali pano komanso m’tsogolo.—Yohane 3:16.

 Kaya munapezekapo pa Cikumbutso ca caka cino kapena ayi, kodi mungapindule bwanji na nsembe ya imfa ya Yesu? Iye anaphunzitsa kuti tiyenela kucita zinthu ziŵili zofunika izi:

  1.  1. Phunzilani za Mulungu komanso Yesu. Popemphela kwa Atate wake wakumwamba, Yesu anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziŵa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”—Yohane 17:3.

  2.  2. Seŵenzetsani zimene mukuphunzila. Yesu anagogomeza kuti tiyenela kuseŵenzetsa zimene anaphunzitsa mu umoyo wathu. Mwacitsanzo, pomaliza Ulaliki wake wochuka wa pa Phili, Yesu anayamikila onse ‘omva mawu ake na kuwacita.’ (Luka 6:46-48) Mofananamo, pa cocitika cina, Yesu anati: “Ngati zimenezi mukuzidziŵa, ndinu odala mukamazicita.”—Yohane 13:17.

 Kodi mungakonde kuphunzila zambili za Mulungu na Yesu? Kodi mukufuna malangizo okuthandizani mmene mungaseŵenzetsele zimene mukuphunzila? Nazi njila zina zimene zingakuthandizeni.

Phunzilo la Baibo

 Pulogalamu yathu ya maphunzilo a Baibo okambilana yathandiza anthu ambili kuisanthula Baibo na kuiseŵenzetsa pa umoyo wawo.

  •   Pitani pa tsamba lakuti Kuphunzila Baibo Mothandizidwa ndi Munthu Wina kuti mudziŵe zambili za pulogalamu imeneyi

  •   Onelelani vidiyo yakuti Takulandilani ku Phunzilo Lanu la Baibo kuti muone mmene phunzilo la Baibo limacitikila na Mboni za Yehova.

Misonkhano ya Mboni za Yehova

 Mboni za Yehova zimasonkhana kaŵili pa mlungu kumalo awo olambilila ochedwa Nyumba ya Ufumu. Pa misonkhanoyi timakambilana Baibo na mmene tingaseŵenzetsele zimene imaphunzitsa pa umoyo wathu.

 Aliyense ni wolandilidwa pa misonkhanoyi; simuyenela kucita kukhala Mboni kuti mupezekepo. Malinga na mmene zinthu zilili kwanuko, mungasankhe kupezeka pa misonkhanoyi pamasom’pamaso kapena pa vidiyokonfalensi.

  •   Tambani vidiyo yakuti N’ciani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu? kuti muone zimene mungayembekezele pa misonkhano imeneyi.

Nkhani za pa intaneti komanso mavidiyo

 Nkhani zambili na mavidiyo pa webusaiti ino zingakuthanzeni kuphunzila zimene Yesu anaphunzitsa na kufunika kwa nsembe yake.

 Mwacitsanzo, kuti mudziŵe mmene imfa ya munthu mmodzi imapindulila anthu mamiliyoni, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi Yesu Amatipulumutsa Bwanji?” komanso yakuti “N’cifukwa Ciani Yesu Anavutika Ndi Kufa?” kapena tambani vidiyo yakuti N’cifukwa Ciani Yesu Anafa?