Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Comstock Images/Stockbyte via Getty Images

KHALANI MASO!

Mudzasankha Ndani Kukhala Mtsogoleli Wanu?—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

Mudzasankha Ndani Kukhala Mtsogoleli Wanu?—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

 M’milungu ingapo ikubwelayi, kudzakhala masankho m’mayiko osiyana-siyana. Palipano, anthu akuganizilapo mwamphamvu kuti adzasankha ndani kukhala mtsogoleli wawo.

 Kodi Baibo ikutipo ciyani?

Atsogoleli aumunthu ni opeleŵela

 Baibo ionetsa kupeleŵela kumene atsogoleli onse aumunthu ali nako.

  •   “Musamakhulupilile anthu olemekezeka, kapena mwana wa munthu wina aliyense wocokela kufumbi amene alibe cipulumutso. Mzimu wake umacoka, ndipo iye amabwelela kunthaka. Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimathelatu.”—Salimo 146:3, 4, mawu a m’munsi.

 Ngakhale atsogoleli ocita bwino kwambili amamwalila m’kupita kwa nthawi. Kuwonjezela apo, owaloŵa m’malo amatha kusintha nchito zabwino zimene iwo anasiya.—Mlaliki 2:18, 19.

 Zoona n’zakuti Baibo ionetsa kuti anthu sanapangidwe kuti azidzilamulila okha.

  •   “Munthu amene akuyenda alibe ulamulilo wowongolela mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.

 Koma kodi alipo amene angapeleke utsogoleli wabwino masiku ano?

Mtsogoleli wosankhidwa na Mulungu

 Baibo imatiuza kuti Mulungu anasankha mtsogoleli wabwino komanso wodalilika kuposa wina aliyense. Mtsogoleli ameneyo ni Yesu Khristu. (Salimo 2:6) Iye ni Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, umene ni boma limene likulamulila kucokela kumwamba.—Mateyu 6:10.

 Kodi mudzasankha Yesu kukhala mtsogoleli wanu? Baibo imaonetsa kuti funso limeneli ni lofunika kwambili.

  •   “Psompsonani mwanayo [Yesu Khristu] kuopela kuti Mulungu angakwiye, Ndipo mungawonongeke ndi kucotsedwa panjilayo. Pakuti mkwiyo wake umatha kuyaka mofulumila. Odala ndi onse amene akuthawila kwa iye.”—Salimo 2:12.

 Ino ndiyo nthawi imene muyenela kusankha. Maulosi a m’Baibo aonetsa kuti Yesu anayamba kulamulila m’caka ca 1914, ndiponso kuti posacedwa Ufumu wa Mulungu udzaloŵa m’malo maboma onse a anthu.—Danieli 2:44.

 Kuti mudziŵe zambili za mmene mungaucilikizile ulamulilo wa Yesu, welengani nkhani yakuti “Sankhani Kucilikiza Ufumu wa Mulungu Palipano!