Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

JenkoAtaman/stock.adobe.com

KHALANI MASO!

Zifukwa Zokhalila na Ciyembekezo mu 2023—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

Zifukwa Zokhalila na Ciyembekezo mu 2023—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

 Pamene taloŵa m’caka ca 2023, tonse timafuna kuti zinthu zitiyendele bwino pamodzi na mabanja athu. Kodi n’cifukwa ciyani tiyenela kukhala na ciyembekezo?

Baibo imatipatsa ciyembekezo

 Baibo imatiuza nkhani yabwino yakuti, mavuto onse amene tikukumana nawo ni a pakanthawi cabe, adzatha posacedwa. Ndiiko komwe, Baibo inalembedwa kuti. . . Itipatse ciyembekezo na kutilimbikitsa.Aroma 15:4.

Ciyembekezo cimene cingakuthandizeni pali pano

 Ciyembekezo cimene Baibo imatipatsa “cili ngati nangula.” (Aheberi 6:19,) Ciyembekezo cimeneco cimatipangitsa kukhala okhazikika, cimatithandizanso kupilila mavuto omwe tikukumana nawo pali pano, kukhala na kapenyedwe kabwino ka zinthu, komanso kupeza cimwemwe cokhalitsa. Mwacitsanzo:

  •   Onani mmene ciyembekezo comwe Baibo imapeleka cinathandizila munthu wina yemwe anali cidakwa. Tambani vidiyo yakuti ’N’nafika Poipidwa ndi Khalidwe Langa.

  •   Onaninso mmene ciyembekezo ca m’Baibo cingatithandizile pamene tayikilidwa wokondedwa wathu mu imfa. Tambani vidiyo yakuti Citonthozo kwa Ofeledwa.

Limbikitsani ciyembekezo canu

 Anthu ambili amakhala na ciyembekezo ca zinthu zabwino, koma sakhala otsimikiza ngati zinthuzo zidzacitikadi. Koma sizili telo na malonjezo a m’Baibo. Cifukwa ciyani? Cifukwa malonjezo a m’Baibo ni ocokela kwa Mulungu a mwini wakeyo, “amene sanganame.” (Tito 1:2) Ni Yehova yekhayo amene amatha kukwanilitsa malonjezo ake onse; ndipo ‘ciliconse cimene Yehova amafuna kucita cimacitika.’—Salimo 135:5, 6.

 Conco pezani ciyembekezo cokupindulilani ca m’Baibo. Mungakulitsenso cidalilo canu pa Baibo mwa kufufuza Malemba mosamala tsiku na tsiku. (Machitidwe 17:11) Kuti mudziŵe bwino zimenezi, pemphani kuti wa Mboni aziphunzila nanu Baibo kwaulele. Inde, ciloweni na ciyembekezo caka ca 2023!

a Yehova ndilo dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.