Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Kodi “mkazi” wochulidwa pa Yesaya 60:1 ndani, nanga ‘adzaimilila’ motani, ndipo ‘adzaonetsa kuwala kwake’ motani?

Pa Yesaya 60:1 timaŵelengapo kuti: “Imilila mkazi iwe! Onetsa kuwala kwako, cifukwa kuwala kwako kwafika. Ulemelelo wa Yehova wakuunikila.” Nkhani yonse ionetsa kuti “mkazi” ni Ziyoni kapena kuti Yerusalemu, mzinda womwe unali likulu la Yuda pa nthawiyo. a (Yes. 60:14; 62:​1, 2) Mzindawo unali kuimilako mtundu wonse wa Isiraeli. Mawu a Yesaya amenewa amautsa mafunso aŵili awa: Loyamba, ni liti komanso motani pomwe Yerusalemu ‘anaimilila’ na kuonetsa kuwala kwauzimu? Laciŵili, kodi kukwanilitsika kwakukulu kwa mawu a Yesaya amenewa kukucitika masiku ano?

Ni liti komanso motani pomwe Yerusalemu ‘anaimilila’ na kuonetsa kuwala kwauzimu? Yerusalemu na kacisi wake anakhalabe matongwe pomwe Ayuda anali ku ukapolo ku Babulo kwa zaka 70. Koma pomwe Amedi na Aperisiya anagonjetsa Babulo , Aisiraeli omwe anali kukhala m’zigawo zonse za Babulo anakhala na mwayi komanso ufulu wobwelela ku dziko lakwawo na kubwezeletsa kulambila koona. (Ezara 1:​1-4) Kuyambila mu 537 B.C.E., Ayuda okhulupilika a mafuko onse 12 anayamba kubwelela ku Yerusalemu na kubwezeletsa kulambila koona. (Yes. 60:4) Anayamba kupeleka nsembe kwa Yehova, kucita zikondwelelo, na kumanganso kacisi. (Ezara 3:​1-4, 7-11; 6:​16-22) Cotelo ulemelelo wa Yehova unayambilanso kuwala pa Yerusalemu—kutanthauza pa anthu amene anabwelela kucokela ku ukapolo. Conco, iwo anakhala kuwala kophiphilitsa kwa mitundu imene inali mu mdima wauzimu.

Komabe maulosi a Yesaya onena za kubwezeletsedwa, anangokwanilitsidwa pa mlingo wocepa cabe pa Yerusalemu wakale. Aisiraeli ambili sanapitilize kumvela Mulungu. (Neh. 13:27; Mal. 1:​6-8; 2:​13, 14; Mat. 15:​7-9) Patapita nthawi, iwo anafika ngakhale pokana Mesiya, Yesu Khristu. (Mat. 27:​1, 2) Mu 70 C.E., Yerusalemu na kacisi wake anawonongedwa kaciŵili.

Yehova ananenelatu za cocitika cimeneci. (Dan. 9:​24-27) N’zoonekelatu kuti Yehova sanafune kuti Yerusalemu wa padziko lapansi akwanilitse mbali zonse za kubwezeletsedwa kwa zimene zinaloseledwa mu Yesaya caputa 60.

Kodi mawu a Yesaya akukwanilitsidwa pa mlingo waukulu masiku ano? Inde, koma akukwanilitsidwa kwa mkazi wina wophiphilitsa—“Yerusalemu wam’mwamba.” Mtumwi Paulo anali kunena za mkaziyu pomwe analemba kuti: “Ndi mayi athu.” (Agal. 4:26) Yerusalemu wam’mwamba ni mbali ya kumwamba ya gulu Mulungu, yopangidwa na zolengedwa zauzimu zokhulupilika. “Ana” a mkaziyu aphatikizapo Yesu komanso Akhristu odzozedwa okwanila 144,000 amene monga Paulo ali na ciyembekezo cokakhala na moyo kumwamba. Akhristu odzozedwa amapanga “mtundu woyela,” kapena kuti “Isiraeli wa Mulungu.”—1 Pet. 2:9; Agal. 6:16.

Kodi Yerusalemu wam’mwamba ‘anaimilila’ motani, nanga anaonetsa ‘kuwala kwake’ motani? Anacita zimenezo kudzela mwa ana ake odzozedwa a padziko lapansi. Onani kugwilizana kumene kulipo pakati pa zimene zinawacitikila na zimene zinaloseledwa mu Yesaya caputa 60.

Akhristu odzozedwa anafunika ‘kuimilila’ cifukwa m’zaka za zana laciŵili C.E., iwo anali ataloŵa mumdima wauzimu, pomwe mpatuko womwe unaloseledwa unali utafalikila panthawiyo. (Mat. 13:​37-43) Conco, iwo analoŵa mu ukapolo kwa Babulo Wamkulu, ufumu wa padziko lonse wa cipembedzo conyenga. Akhristu odzozedwa anakhalabe mu ukapolowo mpaka “mapeto a nthawi ino,” nthawi imene inayamba m’caka ca 1914. (Mat. 13:​39, 40) Pasanapite nthawi, anamasulidwa ku ukapolowo mu 1919. Atangomasulidwa, iwo anayamba kuonetsa kuwala kwawo kwauzimu podzipeleka na mtima wonse pa nchito yolalikila. b Kwa zaka zambili, anthu ocokela m’mitundu yonse abwela mu kuwala kwauzimu kumeneko, kuphatikizapo otsalila a Isiraeli wa Mulungu, omwe ni “mafumu” ochulidwa pa Yesaya 60:3.—Chiv. 5:​9, 10.

Kutsogoloku, Akhristu odzozedwa adzaonetsa kuwala kwa Mulungu pa mlingo wokulilapo. Motani? Mkhristu wodzozedwa akamaliza moyo wake wa padziko lapansi amakakhala mbali ya “Yerusalemu Watsopano,” ndipo amakagwilizana na a 144,000 anzake amene amapanga mkwatibwi wa Khristu wopangidwa na mafumu komanso ansembe. Mzinda wophiphilitsa umenewu umene “ukutsika kucokela kumwamba kwa Mulungu,” ukukhala likulu la gulu la kumwamba la Yehova—“Yerusalemu wam’mwamba.”—Chiv. 14:1; 21:​1, 2, 24; 22:​3-5.

Yerusalemu watsopano adzacita mbali yaikulu kwambili pa kukwanilitsidwa kwa ulosi wa pa Yesaya 60:1. (Yelekezelani Yesaya 60:​1, 3, 5, 11, 19, 20 na Chivumbulutso 21:​2, 9-11, 22-26.) Ku Yerusalemu wakale n’kumene kunali kukhala mafumu olamulila mu Isiraeli. Mofananamo, Yerusalemu watsopano pamodzi na Khristu ndiwo adzakhala mafumu olamulila m’dongosolo la zinthu latsopano. Kodi Yerusalemu watsopano adzatsika motani “kucokela kumwamba kwa Mulungu”? Mwa kucita zinthu zimene zidzakhudza dziko lonse lapansi. “Kuwala kwake kudzaunikila njila” ya anthu a Mulungu ocokela m’mitundu yonse. Ndipo iwo adzamasulidwa ku ucimo na imfa. (Chiv. 21:​3, 4, 24) Zotsatila zake n’zakuti, nthawi imeneyo idzakhala “nthawi yobwezeletsa zinthu zonse” mogwilizana na zimene zinaloseledwa kudzela mwa Yesaya komanso aneneli ena. (Mac. 3:21) Kubwezeletsa zinthu kumeneko kunayamba pomwe Khristu anakhala Mfumu, ndipo kudzatha kumapeto kwa ulamulilo wake wa Zaka Cikwi.

a Pa Yesaya 60:​1, Baibulo la Dziko Latsopano linaseŵenzetsa mawu akuti “mkazi” m’malo moseŵenzetsa mawu akuti “Ziyoni kapena “Yerusalemu.” Anasankha kucita zimenezi cifukwa mawu Aciheberi amene anawamasulila kuti “imilila” komanso akuti “onetsa kuwala” asonyeza kuti amakamba za munthu wamkazi amene akuchulidwa kuti “iwe.” Mawu akuti “mkazi” amathandiza amene akuŵelenga kuzindikila kuti mawu a mlembali akukamba za mkazi.

b Kubwezeletsa zinthu kwauzimu kumene kunacitika mu 1919 kumafotokozedwanso pa Ezekieli 37:​1-14, komanso pa Chivumbulutso 11:​7-12. Ezekieli ananenelatu za kubwezeletsedwa kwauzimu kwa Akhristu onse odzozedwa pambuyo pokhala akapolo kwa nthawi yaitali. Ulosi wa mu Chivumbulutso umakamba za kubadwa kwauzimu kwa kagulu ka abale odzozedwa amene anayamba kutsogolela pambuyo polekeza kutumikila Yehova mokangalika cifukwa coikidwa m’ndende mopanda cilungamo. Mu 1919, iwo anaikidwa kukhala “kapolo wokhulupilika komanso wanzelu.”—Mat. 24:45; onani buku lacingelezi lakuti Pure Worship of Jehovah—Restored At Last!, tsamba 118.