Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi mungathandizeko ena mosasamala kanthu za msinkhu, dziko, kapena cipembedzo cawo?

Madalitso kwa Amene Amathandiza Ofunikila Thandizo

Madalitso kwa Amene Amathandiza Ofunikila Thandizo

Zungulile dziko lapansi, anthu ambili alibe cakudya na nyumba. Ena amafuna cabe kukhala na ciyembekezo ca zakutsogolo. Kodi kuthandiza anthu otelo kungatipangitse bwanji kukhala oyanjidwa na Mulungu, komanso kulandila madalitso ake?

ZIMENE MALEMBA OYELA AMAKAMBA

“Wokomela mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova, ndipo adzam’bwezela zimene anacitazo.”—MIYAMBO 19:17.

ZIMENE KUTHANDIZA WOFUNIKILA THANDIZO KUMATANTHAUZA

Yesu anafotokoza fanizo lokhudza munthu wina amene anavulazidwa ndi acifwamba na kumusiya atatsala pang’ono kufa. (Luka 10:29-37) Koma munthu wina wacilendo anaimilila, na kusamalila munthuyo amene anavulazidwa kwambili. Iye anacita zimenezi ngakhale kuti anali osiyana mtundu na munthuyo.

Munthu wokoma mtima ameneyo anapeleka cithandizo coyambilila ca cipatala kwa munthu wovulazidwayo, na kum’thandiza pa zofunikila zake kuthupi, komanso kum’tonthoza pavuto lake.

Kodi tiphunzilapo ciani pa fanizoli? Yesu anaonetsa kuti tiyenela kuyesetsa kuthandiza ofunikila thandizo mulimonse mmene tingathele. (Miyambo 14:31) Malemba Oyela amaphunzitsa kuti posacedwa, Mulungu adzacotsapo umphawi na mavuto. Koma mwina tingadzifunse kuti, kodi Mulungu adzawacotsapo motani mavuto komanso liti? Nkhani yotsatila idzafotokoza madalitso amene Mlengi wathu wacikondi watisungila.