Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

N’cifukwa Ciani Timakalamba na Kufa?

N’cifukwa Ciani Timakalamba na Kufa?

SICINALI colinga ca Mulungu kuti anthufe tizifa. Makolo athu oyamba Adamu na Hava, analengedwa na maganizo komanso matupi angwilo, ndipo sembe akalipo mpaka lelo. Tidziŵa zimenezi tikaona zimene Yehova anauza Adamu zokhudza mtengo wina wake umene unali m’munda wa Edeni.

Mulungu anauza Adamu kuti: “Tsiku limene udzadya [zipatso za mtengowo], udzafa ndithu.” (Genesis 2:17) Adamu akanalengedwa kuti azikalamba na kufa, sembe lamulo limeneli linalibe tanthauzo. Adamu anali kudziŵa kuti akanasunga lamulo loletsa kudya zipatso za mtengowo, sakanafa.

SICINALI COLINGA CA MULUNGU KUTI ANTHUFE TIZIFA

Kwa Adamu na Hava, panalibe cifukwa codyela zipatso za mtengo woletsedwawo. M’munda wa Edeni munali mitengo ya zipatso yambili-mbili. (Genesis 2:9) Sembe Adamu na Hava sanadye zipatso za mtengowo, iwo akanaonetsa kuti anali omvela kwa Mulungu amene anaŵapatsa moyo. Akanaonetsanso kuti anali kuzindikila mphamvu zimene Mulungu ali nazo zouza anthu zocita.

CIFUKWA CAKE ADAMU NA HAVA ANAFA

Kuti timvetsetse cifukwa cake Adamu na Hava anafa, tifunika kumvetsetsa makambilano amene amatikhudza ife tonse. Satana Mdyelekezi anagwilitsila nchito njoka kuti ikambe bodza lamkunkhuniza. Baibo imati: “Tsopano njoka inali yocenjela kwambili kuposa nyama zonse zakuchile zimene Yehova Mulungu anapanga. Ndipo njokayo inafunsa mkaziyo kuti: ‘Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?’”—Genesis 3:1.

Hava poyankha anati: “Zipatso za mitengo yonse ya m’mundamu anatiuza kuti tizidya. Koma zipatso za mtengo umene uli pakati pa munda, Mulungu anati, ‘Musadye zipatso zake ayi, musaukhudze kuti mungafe.’” Kenako njoka ija inauza Hava kuti: “Kufa simudzafa ayi. Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye cipatso ca mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.” Mwa ici, Satana anakamba kuti Yehova ni wabodza, ndipo anali kumana makolo athu oyamba cinthu cina cabwino.—Genesis 3:2-5.

Hava anakhulupilila zimene anamvela. Atauyang’anitsitsa mtengowo, unaoneka wokhumbilika kwambili m’maso mwake, komanso wolakalakika! Zitatelo, anatambasula dzanja lake na kuthyola zipatso za mtengowo n’kudya. Baibo imati: “Pambuyo pake, anapatsako mwamuna wake pamene anali limodzi, ndipo nayenso anadya.”—Genesis 3:6.

Mulungu anauza Adamu kuti: “Tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.”—GENESIS 2:17

Izi ziyenela kuti zinam’khumudwitsa kwambili Mulungu kuona kuti ana ake okondedwawo, asankha mwadala kusamumvela! Kodi iye anacita ciani? Kwa Adamu, Yehova anati: ‘Udzabwelela kunthaka, pakuti n’kumene unatengedwa. Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwelela.’ (Genesis 3:17-19) Pa cifukwa cimeneci, “masiku onse amene Adamu anakhala ndi moyo anakwana zaka 930, kenako anamwalila.” (Genesis 5:5) Adamu sanayende kumwamba kapena ku dziko la mizimu atamwalila. Yehova akalibe kumulenga kucokela ku dothi, iye kunalibe. Conco pamene anamwalila, anakhala wopanda moyo monga dothi imene Mulungu anaseŵenzetsa pomulenga. Iye tsopano kunalibe. Zinali zomvetsa cisoni kwambili!

CIFUKWA CAKE NDIFE OPANDA UNGWILO

Cifukwa cakuti Adamu na Hava sanamvele Mulungu mwadala, iwo anataya ungwilo komanso ciyembekezo cokhala na moyo wamuyaya. Matupi awo anasintha n’kukhala opanda ungwilo ndi ocimwa. Koma kucimwa kwawo mwa kusamvela Mulungu sikunakhudze iwo okha. Iwo anapatsilako ana awo kupanda ungwiloko. Aroma 5:12 imati: “Monga mmene ucimo unalowela m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa kudzela mwa ucimo, imfayo n’kufalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa.”

Baibo imafotokoza ucimo na imfa kuti zili monga “cophimba cimene cikuphimba anthu onse, ndi nsalu imene yakuta mitundu yonse.” (Yesaya 25:7) Cophimba cimeneci cili monga mphepo ya poizoni, imene palibe angaithaŵe. Kukamba zoona, “mwa Adamu onse akufa.” (1 Akorinto 15:22) Koma funso imene ikhalapo, ni imene mtumwi Paulo anafunsa yakuti: “Ndani adzandipulumutse ku thupi limene likufa imfa imeneyi?” Kodi pali aliyense angakhale mpulumutsi?—Aroma 7:24.