Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?
Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?
ANTHU ENA AMAKHULUPILILA kuti Ufumu wa Mulungu ni mtima wa munthu. Ena amaganiza kuti ni mtendele umene anthu adzabweletsa padziko lonse. Inu muganiza bwanji?
ZIMENE BAIBULO IMAKAMBA
“M’masiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. . . . Koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo [a anthu], ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.” (Danieli 2:44) Ufumu wa Mulungu ndi boma leni-leni.
MFUNDO ZINA ZIMENE BAIBULO IMAKAMBA
Ufumu wa Mulungu uli kumwamba ndipo ukulamulila.—Mateyu 10:7; Luka 10:9.
Mulungu amaseŵenzetsa Ufumu umenewo kuti akwanilitse cifunilo cake kumwamba na padziko lapansi.—Mateyu 6:10.
Kodi Ufumu wa Mulungu Udzabwela Liti?
MUNGAYANKHE BWANJI?
Palibe amene adziŵa
Posacedwa
Sudzabwela
ZIMENE BAIBULO IMAKAMBA
“Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) Uthenga wabwino ukalalikidwa mokwanila, Ufumu wa Mulungu udzabwela kudzaononga dziko loipali.
MFUNDO ZINA ZIMENE BAIBULO IMAKAMBA
Palibe munthu aliyense padziko lapansi amene adziŵa tsiku limene Ufumu wa Mulungu udzabwela.—Mateyu 24:36.
Maulosi a m’Baibulo amaonetsa kuti Ufumu wa Mulungu udzabwela posacedwa.—Mateyu 24:3, 7, 12.