Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Matenda a Maganizo ni Mlili wa Padziko Lonse

Matenda a Maganizo ni Mlili wa Padziko Lonse

“Nthawi zonse nimakhala na nkhawa ngakhale pamene nili khale nekha m’nyumba.”

“Pamene nasangalala kwambili, m’pamenenso nimakhala na nkhawa. Nimadziŵa kuti nikasangalala kwambili, posakhalitsa zinthu zisintha ndipo nikhala wacisoni kwambili.”

“Nimayesetsa kupewa kudela nkhawa za mawa. Koma nthawi zina nimakhala na nkhawa kwambili.”

Mawu amenewa anakambidwa na anthu amene akudwala matenda a maganizo. Kodi umu ni mmene inu kapena munthu wina amene mumam’konda amamvela?

Ngati n’conco, dziŵani kuti simuli nokha. Anthu ambili masiku ano akuvutika na matenda a maganizo. Ndipo ena ali na anzawo kapena acibale amene ali na vuto limeneli.

N’zosacita kufunsa kuti tikukhala ‘m’nthawi yapadela komanso yovuta,’ imene ikupangitsa kuti pakhale mavuto ambili. (2 Timoteyo 3:1) Pa kafukufuku wina anapeza kuti pafupifupi munthu mmodzi pa anthu 8 alionse padziko lonse, amavutika na matenda a maganizo. Komanso cifukwa ca mlili wa COVID-19, mu 2020, ciŵelengelo ca anthu amene anali na vuto la kuda nkhawa kwambili cinawonjezeka na 26 pelesenti. Ndipo ciŵelengelo ca anthu odwala matenda ovutika maganizo cinawonjezeka na 28 pelesenti.

Kudziŵa ciŵelengelo ca anthu amene akudwala matenda ovutika maganizo n’kofunika. Koma cofunika kwambili ni kudziŵa mmene inu na okondedwa anu mungasamalile thanzi lanu.

Kodi thanzi la maganizo n’ciyani?

Munthu amene ali na thanzi la maganizo amakhala na mtendele wa mumtima, komanso amacita zinthu zolongosoka. Amatha kulimbana na nkhawa za tsiku na tsiku, kugwila nchito bwino-bwino, komanso kukhala wacimwemwe.

Matenda a maganizo

  • SAMABWELA cifukwa cakuti munthu ni wopeleŵela penapake.

  • Ni matenda ndithu amene amapangitsa munthu kukhala wopanikizika kwambili, ndipo amamulepheletsa kuganiza bwino, kulamulila mtima wake, na kucita zinthu bwino-bwino.

  • Nthawi zambili matendawa amalepheletsa munthu kupanga ubwenzi na ena. Amamulepheletsanso kugwila bwino nchito za tsiku na tsiku.

  • Munthu aliyense angadwale matenda amenewa mosasamala kanthu za msinkhu wake, mtundu, cikhalidwe, cipembedzo, maphunzilo, kapenanso kuti kaya ni wolemela kapena wosauka.

Kumene odwala matenda a maganizo angapeze thandizo

Nthawi zina, munthu angasinthe mwadzidzidzi mmene amacitila zinthu. Angayambe kugona kwambili kapena kusoŵa tulo, kudya kwambili kapena kusafuna kudya. Mwinanso angayambe kukhala na nkhawa kwambili kapena cisoni. Zikakhala conco, munthuyo angafunike kuonana na odziŵa za matenda a maganizo kuti adziŵe cimene cikupangitsa vutolo na kulandila thandizo. Koma kodi n’kuti maka-maka kumene angapeze thandizo?

Yesu Khristu, amene anali wanzelu kwambili kuposa onse amene anakhalako, anati: “Anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.” (Mateyu 9:12) Anthu odwala matenda a maganizo akalandila thandizo loyenelela lacipatala, vuto lawo lingacepeko moti angakhalenso na umoyo waphindu komanso wacimwemwe. Anthu otelo sayenela kucedwa kulandila thandizo ngati vuto lawo n’lalikulu, kapena ngati zizindikilo zimatenga nthawi yaitali. a

Ngakhale kuti Baibo si buku la malangizo a zacipatala, zimene imakamba zingatithandize ngati tikudwala matenda a maganizo. Conde ŵelengani nkhani zotsatilazi, zimene zifotokoza mmene Baibo ingatithandizile ngati tikudwala matenda a maganizo.

a Magazini ya Nsanja ya Mlonda siisankhila anthu thandizo la mankhwala. Munthu aliyense ayenela kufufuza mosamala thandizo la mankhwala limene angalandile, kenako n’kudzipangila cisankho.