Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mulungu N’ndani?

Kodi Mulungu N’ndani?

Ambili amakamba kuti amakhulupilila Mulungu. Koma mukaŵafunsa kuti Mulungu n’ndani, iwo amapeleka mayankho osiyana-siyana. Anthu ena amakamba kuti Mulungu ni woweluza wankhanza, amene amakhalila cabe kulanga anthu pa zolakwa zawo. Ena amakhulupilila kuti nthawi zonse ni wacikondi komanso wokhululuka olo acite zoipa bwanji. Ndipo enanso amakhulupilila kuti Mulungu ali kutali kwambili na kuti sasamala za ise. Popeza anthu ali na malingalilo osiyana-siyana pa nkhaniyi, ambili amaona kuti n’zosatheka kum’dziŵa bwino Mulungu.

Kodi kum’dziŵa Mulungu n’kofunika? Inde, n’kofunika. Kum’dziŵa bwino Mulungu kungakuthandizeni kukhala na umoyo waphindu komanso wa colinga. (Machitidwe 17:26-28) Mukamuyandikila kwambili, m’pamenenso adzakukondani na kukuthandizani. (Yakobo 4:8) Ndipo kum’dziŵa bwino Mulungu, kudzakuthandizani kuti mukapeze moyo wopanda mapeto.—Yohane 17:3.

Kodi mungam’dziŵe bwanji Mulungu? Ganizilani mnzanu wapamtima amene mumam’dziŵa bwino kwambili. Kodi ubwenzi wanu unayamba bwanji? Mwacionekele munafuna kudziŵa dzina lake, umunthu wake, zimene amakonda na zimene sakonda. Ndipo munafunanso kudziŵa zinthu zina zimene anacitapo m’mbuyomo na zimene afuna kucita, na zina zaconco. Izi n’zimene zinakupangitsani kuti mufike pom’konda munthuyo. Inde, munadziŵa zambili za iye.

Ngakhale ise, tingam’dziŵe bwino Mulungu mwa kupeza mayankho pa mafunso aya:

Colinga ca magazini ino, nikupeleka mayankho a m’Baibo pa mafunso monga amenewa. Ndipo nkhani za m’magazini ino zidzakuthandizani kum’dziŵa bwino Mulungu, komanso mmene mungapindulile mukakhala naye pa ubwenzi wabwino.