Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Cidziŵitso Cimene Cimatithandiza Kukhala Mabwenzi a Mulungu

Cidziŵitso Cimene Cimatithandiza Kukhala Mabwenzi a Mulungu

Sikuti Mlengi wathu ni mphamvu cabe yopanda moyo. Koma ni Mulungu weniweni amene ali na makhalidwe abwino. Ndipo amafuna kuti tim’dziŵe na kukhala naye paubwenzi. (Yohane 17:3; Yakobo 4:8) Ndiye cifukwa cake watiuza zambili zokhudza iye.

Mlengi Wathu Ali na Dzina

“Kuti anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulila dziko lonse lapansi.”—SALIMO 83:18.

Baibo imaphunzitsa kuti Yehova ndiye Mulungu yekha woona. Iye ndiye analenga cilengedwe conse na zamoyo zonse. Tiyenela kulambila iye cabe.—Chivumbulutso 4:11.

Yehova Ni Mulungu Wacikondi

“Mulungu ndiye cikondi.”—1 YOHANE 4:8.

Kupitila m’Baibo komanso zinthu zimene analenga, Yehova amatiphunzitsa makhalidwe ake ambili. Khalidwe lake lalikulu ni cikondi. Iye amacita zinthu zonse cifukwa ca cikondi. Tikaphunzila zambili za Yehova, timafika pom’konda kwambili.

Yehova Ni Mulungu Wokhululuka

“Inu ndinu Mulungu wokhululuka”—NEHEMIYA 9:17.

Yehova amadziŵa kuti ndife opanda ungwilo. Conco amakhala wokonzeka kutikhululukila. Tikavomeleza kulakwa kwathu na kuyesetsa kuleka kucita zinthu zoipa, iye adzatikhululukila ndipo sadzatipatsanso cilango cifukwa ca macimo amene tinalapa.—Salimo 103:12, 13.

Yehova Amafuna Kuti Tizipemphela kwa Iye

“Yehova ali pafupi ndi onse oitanila pa iye . . . Adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo.”—SALIMO 145:18, 19.

Yehova safuna kuti pomulambila tizicita miyambo yapadela kapena kuseŵenzetsa mafano na zinthu zina. Iye amamvetsela mapemphelo athu monga mmene makolo acikondi amamvetselela ana awo akamakamba.