Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 8

N’cifukwa Ciani Mulungu Amalolela Kuti Anthu Azivutika?

N’cifukwa Ciani Mulungu Amalolela Kuti Anthu Azivutika?

1. Kodi mavuto anayamba bwanji?

Mulungu walola anthu kulamulila nthawi yaitali kuti awaonetse kuti io sangakwanitse kuthetsa mavuto ao

Mavuto anayamba padziko lapansi pamene Satana anakamba bodza loyamba. Paciyambi asanakhale Satana, iye anali mngelo wangwilo, koma “sanakhazikike m’coonadi.” (Yohane 8:44) Anafuna kuti azilambilidwa m’malo mwakuti Mulungu yekha azilambilidwa. Satana ananama Hava, mkazi woyamba, ndi kum’nyengelela kuti amvele iye m’malo momvela Mulungu. Adamu naye sanamvele Mulungu mofanana ndi Hava. Cosankha ca Adamu cinayambitsa mavuto ndi imfa.​—Ŵelengani Genesis 3:1-6, 19.

Pamene Satana anauza Hava kuti asamvele Mulungu, Satanayo anayamba kupandukila ulamulilo wa Mulungu, kapena kuti udindo wake monga Wam’mwamba-mwamba. Anthu ambili agwilizana ndi Satana pa kukana Mulungu monga Wolamulila wao. Mwa ici, Satana wakhala “wolamulila wa dziko.”​—Ŵelengani Yohane 14:30; 1 Yohane 5:19.

2. Kodi zolengedwa za Mulungu zinali zopanda ungwilo?

Nchito zonse za Mulungu n’zangwilo. Anthu ndi angelo amene Mulungu analenga akanakwanitsa kumvela Mulungu bwino-bwino. (Deuteronomo 32:4, 5) Mulungu anatilenga ndi ufulu wosankha kucita cabwino kapena coipa. Ufulu umenewo umatipatsa mwai woonetsa kuti timakonda Mulungu.​—Ŵelengani Yakobo 1:13-15; 1 Yohane 5:3.

3. N’cifukwa ciani Mulungu walola mavuto mpaka lelo?

Kwa kanthawi, Yehova walola anthu kupandukila ulamulilo wake. N’cifukwa ciani walola zimenezi? Wacita zimenezi kuti aonetse anthu kuti palibe ulamulilo uliwonse umene ungapindulitse anthu popanda iye. (Mlaliki 7:29; 8:9) Koma pambuyo pa zaka 6,000 za mbili ya anthu, umboni waonekelatu wakuti anthu alephela kucotsapo nkhondo, upandu, kupanda cilungamo, kapena matenda.​—Ŵelengani Yeremiya 10:23; Aroma 9:17.

Mosiyana ndi ulamulilo wa anthu, ulamulilo wa Mulungu umapindulitsa anthu amene amauvomeleza. (Yesaya 48:17, 18) Posacedwa, Yehova adzathetsa maboma onse a anthu. Koma anthu amene amasankha kulamulidwa ndi Mulungu ndi amene adzakhala padziko lapansi.​—Yesaya 11:9.—Ŵelengani Danieli 2:44.

Tambani vidiyo N’cifukwa Ciani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?

4. Kodi kuleza mtima kwa Mulungu kwatipatsa mwai wocita ciani?

Satana anakamba kuti anthu amatumikila Yehova pa zifukwa zadyela. Kodi mungakonde kutsutsa bodza limeneli? Zimenezi n’zotheka! Kuleza mtima kwa Mulungu kumatipatsa mwai woonetsa ngati tili kumbali ya ulamulilo wa Mulungu kapena wa munthu. Timaonetsa mbali imene tili mwa zimene timacita.​—Ŵelengani Yobu 1:8-12; Miyambo 27:11.

5. Kodi tingacite ciani kuti Mulungu akhale Wolamulila wathu?

Zosankha zathu zimaonetsa ngati tifuna Mulungu kukhala Wolamulila wathu

Kuti Mulungu akhale Wolamulila wathu tiyenela kuphunzila za kulambila koona kozikidwa m’Mau a Mulungu Baibo, ndi kucita zinthu mogwilizana ndi kulambila kumeneko. (Yohane 4:23) Tingam’kane Satana kuti asakhale wolamulila wathu mwa kusatenga mbali m’ndale ndi m’nkhondo, monga mmene Yesu anacitila.​—Ŵelengani Yohane 17:14.

Satana amagwilitsila nchito mphamvu zake kulimbikitsa makhalidwe oipa ndi oononga. Tikaleka makhalidwe amenewo, anzathu ena ndi acibanja angatinyoze kapena kutitsutsa. (1 Petulo 4:3, 4) Conco tiyenela kusankhapo. Kodi tidzayanjana ndi anthu amene amakonda Mulungu? Kodi tidzamvela malamulo ake anzelu ndi acikondi? Tikacita zimenezo, tidzaonetsa kuti Satana ananena bodza pamene anati palibe munthu amene angamvele Mulungu pamene akumana ndi mavuto.​—Ŵelengani 1 Akorinto 6:9, 10; 15:33.

Cikondi ca Mulungu kwa anthu cimaonetsa kuti mavuto adzatha. Anthu amene amaonetsa kuti amakhulupilila zimenezi adzasangalala ndi moyo wamuyaya padziko lapansi.​—Ŵelengani Yohane 3:16.